Mutu-2

1Komatu iwe ulankhule zinthu zimene zimakhala chiphunzitso chabwino; 2kuti okalamba akhale odziletsa, akhalidwe labwino, anzeru, achikhulupiriro cholimba, achikondi, odekha; 3kuti akazi okalamba chimodzimodzi akayende monga oyenera kuphunzitsa iwo akulankhula pa zinthu zopatulika, osati amijedu, osakhala akapolo akumwa vinyo mopyoza, aphunzitsi a zinthu zimene zili zabwino; 4kuti akalangize atsikana akonde amuna awo, akonde ana awo, 5anzeru, oyera, ogwira bwino ntchito za pakhomo, abwino, akumvera amuna a iwo okha, kuti mau a Mulungu1 asalankhulidwe zoipa. 6Chimodzimodzi anyamata uwalimbikitse akhale a nzeru: 7mu zinthu zonse udzionetsere wekha chitsanzo cha ntchito zabwino; m’kuphunzitsa moyenera, makhalidwe abwino, 8mau olamitsa, osatsutsidwa; kuti iye amene akatsutsana nawo akachite manyazi, popanda kulankhula koipa kokhudza ifeyo: 9akapolo akamvere ambuye a iwo okha, kukadzipanga okha kukhala ovomerezeka mu zonse; osalankhula mau otsutsana; 10osabera [ambuye awo], koma poonetsera kukhulupirika konse, kuti akongoletse chiphunzitso chimene chili mwa Mulungu2 mpulumutsi wathu mu zinthu zonse. 11Pakuti chisomo cha Mulungu3 chimene chimanyamula chipulumutso cha anthu onse chaonekera, 12kutiphunzitsa ife kuti, pokana chisapembedzo ndi zilakolako za dziko lapansi, tikakhale odziletsa, ndi olungama, ndi opembedza ndi m’mene zinthu zilili m’dziko tsopano, 13kudikilira chiyembekezo chodala ndi kuonekera kwa ulemelero wa Mulungu4 wathu wamkulu ndi Mpulumutsi Yesu Khristu; 14amene anadzipereka yekha kwa ife, kuti akatiombole ku zoipa zonse, ndi kudziyeretsera yekha anthu opatulika, achangu pa ntchito zabwino. 15 Zinthu izi ulankhule, ndi kulimbikitsa, ndi kudzudzula ndi ulamuliro onse. Usalole aliyense akupeputse iwe.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu