Mutu 9
1Loyambalo pamenepo lili nawo malamulo a utumiki, ndi malo opatulika, a padziko lapansi. 2Pakuti chihema chinakonzedwa; choyamba chija, m’mene munali choikapo nyali ndi gome ndi mkate woonekera, umene umatchedwa Woyera; 3koma kupyola chophimba chihema chachiwiricho chimene chimatchedwa Malo opatulikitsa, 4okhala nacho chofukiza cha golide, ndi likasa la chipangano, lokutidwa mozungulira mbali zonse ndi golide, m’mene munali mphika wa golide umene unali ndi mana, ndi ndodo ya Aroni imene inaphukayo, ndi magome a chipangano; 5ndipo pamwamba pake akerubi a ulemelero kuonetsera mpando wa chifundo; zokhudza izi sitifotokoza tsopano mwatsatanetsatane.
6Tsopano zinthu zimenezi pokhala kuti zinakonzedwa motere, m’chihema choyamba wansembe amalowa nthawi zonse, kukwaniritsa mautumiki; 7koma m’chachiwiricho, mkulu wa ansembe amalowa yekha, kamodzi pachaka, osati popanda mwazi, umene amapereka pa iye yekha ndi zolakwa za anthu: 8Mzimu woyera poonetsera izi, kuti njira yoyeretsetsa sinaonetsedwe pamene chihema choyamba chidakali chilili; 9chimene chili chisonyezo cha nthawi yino, molingana ndi momwe mphatso ndi nsembe, sizinakhoze kulungamitsa monga ku chikumbumtima iye amene wakulambiridwa, anaperekera, 10[zopangidwa] ndi nyama yokha ndi zakumwa ndi zosamba zosiyanasiyana, malamulo atsopano, oyikidwa kufikira nthawi imene zinthu zizayikidwe m’chimake. 11Koma Khristu pakudza mkulu wa ansembe wa zinthu zabwino zili nkudza, mwa ubwino ndi chihema changwiro choposa chosapangidwa ndi dzanja, (ndiko kuti, osati wa m’badwo uno,) 12kapena mwa mwazi wa mbuzi ndi ng’ombe, koma mwa mwazi wake omwe, walowa kamodzi kokha kwatha ku malo oyeretsetsa, atapeza chiombolo chamuyaya. 13Pakuti ngati mwazi wa mbuzi ndi ng’ombe, ndi phulusa la ng’ombe ya mphongo lowazidwa pa iwo odetsedwa, nsembe ya chiyeretso cha thupi, 14nanga koposa kotani udzayeretsa mwazi wa Khristu, amene mwa Mzimu wamuyaya anadzipereka wopanda banga kwa Mulungu1, kuyeretsa chikumbumtima chanu ku ntchito zakufa kukalambira Mulungu2 wa moyo? 15Ndipo pachifukwa chimenechi iye ndi mkhalapakati wa pangano latsopano, kuti, imfa itatenga malo pa chiombolo cha ochimwa pansi pa pangano loyamba lija, oyitanidwa akalandire lonjezano la cholowa chamuyaya. 16(Pakuti kumene kuli chipangano, imfa ya wochitira umboni ikuyenera kufika. 17Pakuti chipangano ndi chokakamiza pamene anthu ali akufa, potero sichidzakhala chokakamiza ngati wochitira umboniyo adakali ndi moyo.) 18Pamenepo choyambacho sichikanakonzedwa popanda mwazi. 19Pakuti lamulo lililonse linalankhulidwa molingana ndi lamulo la Mose kwa anthu onse; pokhetsa mwazi wa ng’ombe ndi mbuzi, ndi madzi ndi ubweya wofiira ndi hisope, anawaza pa bukulo ndi pa anthu onse, 20nanena, Uwu ndi mwazi wa pangano umene Mulungu3 anaulamulira kwa inu. 21Ndi chihemanso ndi ziwiya zonse zotumikilira anaziwazanso chimodzimodzi ndi mwazi; 22ndipo pafupifupi zinthu zonse zayeretsedwa ndi mwazi molingana ndi lamulo, ndipo popanda kukhetsa mwazi kulibe chikhululukiro. 23KunaIi kofunika nthawi imeneyo kuti chifaniziro chophiphiritsa cha zinthu m’mwamba chiyeretsedwe ndi zimenezi; koma zinthu za kumwamba pazokha ndi nsembe ziposa izi. 24Pakuti Khristu sanalowe m’malo oyeretsetsa opangidwa ndi dzanja, ziwerengero, koma zakumwambako, tsopano kuonekera pamaso pa Mulungu4 kwa ife: 25kapena cholinga kuti akadzipereke yekha kawirikawiri, monga mkulu wa ansembe alowa m’malo oyeretsetsa chaka chilichonse ndi mwazi osati iye yekha; 26pakuti iye pamenepo anakakamizidwa kawirikawiri kumva zowawa kuyambira maziko a dziko lapansi. Koma tsopano kamodzi kokha pakutha pa nthawi zonsezi waonetsedwa kukachotsa tchimo mwa nsembe yake. 27Ndipo popeza ili ndilo gawo la anthu kufa kamodzi, ndipo kenako chiweruziro; 28 Kotero Khristunso, ataperekedwa kamodzi kusenza machimo a anthu ambiri, adzaonekera kwa iwo akuyang’ana pa iye kachiwiri popanda tchimo pa chipulumutso.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu