Mutu 6
1Aliyense wa inu, pamene ali ndi mlandu ndi mzake, bwanji apititsa mlandu wake pamaso pa osalungama, ndipo osati pa olungama? 2Kodi simudziwa pamenepo kuti oyera mtima adzaweruza dziko lapansi? Ndipo ngati dziko lapansi liweruzidwa ndi inu, kodi sinu oyenera kuweruza milandu yochepa? 3Kodi inu simudziwa kuti tidzaweruza angelo? Ndipo nanga pamenepo zinthu za moyo uno? 4Pamenepo ngati muli nayo milandu ya zinthu za moyo uno, muyika iwo osawerengedwa mu mpingo kukuweruzani. 5Ndalankhula kwa inu kuti ndikuchititseni manyazi. Kuti palibe munthu wa nzeru pakati panu, ngakhale m’modzi, amene akhoza kuweruza pakati pa abale ake! 6Komatu m’bale anena mlandu wake ndi mnzake, ndipo pamaso pa osakhulupilira. 7Zoonadi chokhacho kuti pamenepo mwapezerana milandu pakati panu mwalakwitsa kale. Chifukwa chiyani simungathe kupilira pa choipa? Chifukwa chiyani osangolola akupusitseni? 8Koma inu muchita choipa, ndi kupusitsa, ndipo muchitira ichi m’bale wanu. 9Kodi simudziwa kuti anthu osalungama sadzalowa ufumu wa Mulungu1? Musanyengeke: adama, kapena opembedza mafano, kapena achigololo, kapena amuna adama, kapena akazi oziyipsa okha ndi amuna, 10kapena akuba, kapena osilira, kapena oledzera, kapena anthu a phuzo, kapena olanda, sadzalowa ufumu wa Mulungu2. 11Ndipo ena mwa inu munali otere; koma mwasambitsidwa, koma mwayeretsedwa, koma mwalungamitsidwa m’dzina la Ambuye Yesu, ndi mwa Mzimu wa Mulungu3.
12Zinthu zonse ndi zololedwa kwa ine, koma sizonse zimene zipindula; zinthu zonse ndi zololedwa kwa ine, koma sindidzakhala pansi pa mphamvu ya chilichonse. 13Chakudya ndicho cha mimba, ndipo mimba ndiyo ya chakudya; Koma Mulungu4 adzaonononga zonsezi: komatu thupi si lachigololo, koma la Ambuye, ndipo Ambuye ndi wa thupili. 14Ndipo Mulungu5 waukitsa Ambuye, ndipo adzatiukitsa ife kuchoka kwa akufa mwa mphamvu yake. 15Kodi simudziwa kuti matupi anu ali ziwalo za Ambuye? Pamenepo kodi, ndidzatenga ziwalo za Khristu, ndi kudzipanga kukhala ziwalo za mkazi wa chiwerewere? Musaganize choncho. 16Kodi simudziwa kuti iye wophatikidwa ndi mkazi wa chiwerewere ali thupi limodzi? Pakuti awiriwa, atero Iye, adzakhala thupi limodzi. 17Koma iye amene aphatikidwa kwa Ambuye ali Mzimu umodzi. 18Thawani dama. Tchimo lililonse limene munthu alichita lili kunja kwa thupi lake, koma iye amene achita chigololo achimwira thupi lake lomwe. 19Kodi simudziwa kuti thupi lanu ndilo kachisi wa Mzimu Woyera amene ali mwa inu, umene muli nawo mwa Mulungu6; ndipo si wainu eni? 206pakuti inu munagulidwa ndi mtengo wake: pamenepo tsopano lemekezani Mulungu7 m’thupi lanu.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu7Elohimu