Mutu 5
1Ndipo ndinaona padzanja lake lamanja la iye wakukhala pa mpando wachifumu buku, lolembedwa mkati ndi kuseri kwake, losindikizidwa ndi zizindikiro zisanu ndi ziwiri. 2Ndipo ndinaona mngelo wamphamvu akulalikira ndi mau akulu, Ndani ali woyenera kutsegula bukuli, ndi kuthyola zizindikiro zake? 3Ndipo palibe m’mwamba, kapena padziko lapansi, kapena pansi dziko, angatsegule bukuli, kapena kulilingalira. 4Ndipo ndinalira kwambiri chifukwa palibe amene anapezeka woyenera kutsegula bukulo kapena kulilingalira. 5Ndipo m’modzi wa akulu anati kwa ine, Usalire. Taona, mkango umene uli wafuko la Yuda, muzu wa Davide, wakwanitsa kutsegula bukuli, ndi zizindikiro zake zisanu ndi ziwiri.
6Ndipo ndinaona pakati pa mpando wachifumu ndi zolengedwa zamoyo zinayi, ndipo pakati pa akulu, Mwanawankhosa atayimilira, monga wophedwa, okhala nazo nyanga zisanu ndi ziwiri ndi maso asanu ndi awiri, ndiyo Mizimu ya Mulungu1 isanu ndi iwiri imene yatumizidwa padziko lonse lapansi: 7ndipo anadza natenga bukulo m’dzanja lamanja la iye wokhala pa mpando wachifumu. 8Ndipo pamene anatenga bukulo, zamoyo zinayizo ndi akulu makumi awiri ndi mphambu anayi anagwa pamaso pa Mwanawankhosa, okhala nawo azeze ndi mbale za golide zodzadza ndi zofukiza, amene ndi mapemphero a oyera mtima. 9Ndipo iwo anayimba nyimbo yatsopano, nanena, Mwayenera inu kutenga bukulo, ndi kutsegula zizindikiro zake; chifukwa inu mwaphedwa, ndipo munawombola kwa Mulungu2, mwa mwazi wanu, kuchokera kwa mitundu yonse, ndi lilime, ndi anthu, ndi mafuko, 10ndipo munawapanga iwo kwa Mulungu3 mafumu ndi ansembe; ndipo adzalamulira dziko lapansi.
11Ndipo ndinaona, ndikumva mau a angelo ochuluka akuzungulira mpando wachifumu ndi zolengedwa zamoyo ndi akulu; ndipo chiwerengero chawo chinali zikwi khumi kuchulukitsanso zikwi khumi ndi zikwi zikwi; 12akunena ndi mau akulu, Wayenera Mwanawankhosa amene waphedwa, kulandira mphamvu, ndi chuma, ndi nzeru, ndi chilimbiko, ndi ulemu, ndi ulemelero, ndi mdalitso. 13Ndipo cholengedwa chilichonse chimene chili m’mwamba ndi padziko lapansi ndi pansi pa dziko, ndi [zimene zili] panyanja, ndi zinthu zonse zili mkati mwake, ndinazimva zikunena, Kwa iye wakukhala pa mpando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa, mdalitso, ndi ulemu, ndi ulemelero, ndi mphamvu, ku nthawi za nthawi. 14 Ndipo zolengedwa za moyo zinayi zinati, Amen; ndipo akulu anagwa pansi nalambira.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu