Mutu 14

1Tsopano pasaka komanso [phwando] la mkate wopanda chotupitsa zimayenera kuchitika pakutha pa masiku awiri. Ndipo akulu ansembe ndi alembi amafuna njira ya momwe angamugwirire Iye mwa chiwembu ndi kumupha. 2Pakuti anati, Osati pa phwando, popeza mwina pakhoza kukhala chisokonezo cha anthu.

3Ndipo pamene Iye anali ku Betaniya, m’nyumba ya Simoni wakhate, pamene anakhala pa gome, anafika mkazi wakukhala nayo nsupa ya alabastero ya mafuta onunkhira bwino a nardo, a mtengo wapatali; ndipo ataphwanya nsupayo, anathira pamutu pa Iye. 4Ndipo analipo ena amene anasautsika mwa iwo okha, nanena, Chifukwa chiyani mafutawa awonongedwa chonchi? 5pakuti mafuta amenewa akanatha kugulitsidwa marupiya opitilira mazana atatu ndi kupereka kwa osauka. Ndipo iwo anamulankhulira mwaukali mkaziyo. 6Koma Yesu anati, Msiyeni iye; chifukwa chiyani mukumvutitsa? Iye wachita ntchito yabwino kwa Ine; 7pakuti osauka muli nawo nthawi zonse, ndipo pamene mufuna mungathe kuwachitira iwo zabwino; koma Ine simuli nane nthawi zonse. 8Chimene iye akanatha kuchita wachichita. Iye wadzozeratu thupi langa kukuikidwa m’manda. 9Ndipo zoonadi ndinena kwa inu, Kulikonse kumene uthenga wabwino udzalalikidwa padziko lapansi, chimene [mkazi] uyu wachita chidzanenedwanso kukhala chikumbukiro kwa iye.

10Ndipo Yudase Iskariote, m’modzi wa khumi ndi awiriwo, anapita kwa akulu ansembe kuti iye akhoza kumpereka kwa iwo; 11ndipo iwo, pamene anamva ichi, anakondwera, ndipo anamulonjeza kumpatsa ndalama. Ndipo iye anafunafuna njira m’mene angamperekere Iye.

12Ndipo tsiku loyamba la mkate wopanda chotupitsa, pamene anapha pasaka, ophunzira ake anati kwa Iye, Kodi mukufuna tipite kuti kukakonzekera, kuti inu mukadye mkate? 13Ndipo Iye anatumiza awiri a ophunzira ake, nati kwa iwo, Pitani mu mzinda, ndipo munthu akakumana nanu atanyamula mtsuko wa madzi; mtsateni iye. 14Ndipo kulikonse kumene iye akalowe, mukanene kwa mwini nyumbayo, Mphunzitsi akuti, Chili kuti chipinda chimene ndikadyere pasaka pamodzi ndi ophunzira anga? 15ndipo iye akakuonetsani chipinda chachikulu chapamwamba chokonzedwa kale. M’menemo tikonzereni ife. 16Ndipo ophunzira ake anachoka ndi kulowa mu mzinda, ndipo anapeza monga umo Iye ananenera kwa iwo; ndipo iwo anakonza pasakayo.

17Ndipo pamene madzulo anafika, Iye anabwera pamodzi ndi khumi ndi awiriwo. 18Ndipo pamene iwo anakonza gome ndi kuseyama, Yesu anati, Ndithudi Ine ndinena kwa inu, M’modzi wa inu adzandipereka Ine; iye amene akudya pamodzi ndi Ine. 19Ndipo iwo onse anayamba kumva chisoni, ndipo anati kwa Iye, m’modzi m’modzi, Kodi ndi ine? [ndi wina, Kodi ndi ine?] 20Koma Iye anayankha nati kwa iwo, M’modzi wa khumi ndi awiri, iye amene akususa pamodzi ndi Ine m’mbale. 21Mwana wa munthu adzapita ndithu monga kunalembedwa zokhudza Iye, koma tsoka kwa munthu amene Mwana wa munthu adzaperekedwa ndi iye; [kukanakhala] kwabwino munthu ameneyu akanapanda kubadwa.

22Ndipo pamene anali nkudya, Yesu pakutenga mkate, pamene anaudalitsa, anaunyema, naupereka kwa iwo, ndipo anati, Tengani: limeneli ndi thupi langa. 23Ndipo atatenga chikho, pamene Iye anayamika, anapereka kwa iwo, ndipo onse anamwera ichi. 24Ndipo Iye anati kwa iwo, Uwu ndi mwazi wanga, umene uli pangano [latsopano], umene unakhetsedwera ambiri. 25Ndithudi ndinena kwa inu, sindidzamwanso za chipatso cha mpesa, kufikira tsiku limene ndidzamwanso kwatsopano mu ufumu wa Mulungu1. 26Ndipo atayimba nyimbo, iwo anapita ku phiri la Azitona.

27Ndipo Yesu anati kwa iwo, Nonsenu mudzakhumudwa, pakuti kwalembedwa, ndidzakantha m’busa ndipo nkhosa zizabalalika. 28Komatu Ine ndikadzauka, ndidzapita patsogolo panu mu Galileya. 29Koma Petro anati kwa Iye, Ngakhale onse adzakhumudwa koma ine ayi. 30Ndipo Yesu anati kwa iye, Ndithudi ndinena kwa iwe, kuti lero lomwelino, usiku uno, tambala asanalire kawiri, udzandikana ine katatu. 31Koma iye analankhula [kwambiri] moonjeza, Ngakhale kufa kumene ndikafa ndi inu. Ndipo chimodzimodzi onse analankhulanso chonchi.

32Ndipo anafika ku malo kumene dzina lake [ndi] Getsemane, ndipo Iye anati kwa ophunzira ake, Khalani pano pamene Ine ndikukapemphera. 33Ndipo Iye anatengana ndi Petro ndi Yakobo ndi Yohane, ndipo Iye anayamba kukhala wodabwa ndi kupsinjika mu mzimu. 34Ndipo anati kwa iwo, Moyo wanga uli wodzala ndi chisoni chofikira ku imfa; bakhalani pano ndi kudikira. 35Ndipo, atapita patsogolo pang’ono, anagwa pansi; ndipo anapemphera kuti, ngati ndi kotheka, nyengo imeneyi imudutse. 36Ndipo Iye anati, Abba, Atate, zinthu zonse zimatheka kwa Inu: chotsani chikho ichi kwa Ine; koma osati chimene Ine ndifuna, komatu chimene Inu [mufuna]. 37Ndipo Iye anabwera nawapeza iwo akugona. Ndipo Iye anati kwa Petro, Simoni, kodi mukugona? Simungathe kudikira kwa ola limodzi? 38Dikirani ndi kupemphera, kuti musalowe m’kuyesedwa. Zoonadi mzimu [uli] wofunitsitsa, koma thupi lofooka. 39Ndipo pakuchoka, Iye anapempheranso, nanena chinthu chomwechi. 40Ndipo pobwerera, Iye anawapezanso iwo akugona, pakuti maso awo anali olemera; ndipo sanadziwe chimene akuyenera kumuyankha Iye. 41Ndipo Iye anabweranso kachitatu nati kwa iwo, Zigonani tsopano, ndipo bapumulani. Kwakwanira; ola lafika; taonani, Mwana wa munthu aperekedwa m’manja mwa anthu ochimwa. 42Dzukani, tiyeni tizipita; taonani, iye wakundipereka Ine wayandikira.

43Ndipo nthawi yomweyo, pamene Iye adakali chilankhulire, Yudase anabwera, [pokhala] iye m’modzi wa khumi ndi awiriwo, pamodzi ndi khamu lalikulu, lokhala ndi malupanga ndi zikwapu, akuchokera kwa akulu ansembe ndi alembi ndi akulu. 44Tsopano iye wakumpereka anawapatsa iwo chizindikiro pakati pawo, nanena, Amene ndidzampsopsona ine, ndi yemweyo; m’gwireni, ndi kumuka naye chisungire. 45Ndipo pakubwera, analunjika chindunji kwa Iye, nati, Rabbi, Rabbi; ndipo anampsopsonetsa Iye. 46Ndipo iwo anaika manja awo pa Iye namgwira. 47Komatu wina wa iwo wakuimilira pamenepo, anatulutsa lupanga lake, nagwaza nalo kapolo wa mkulu wa nsembe, nadula khutu lake. 48Ndipo Yesu poyankha anati kwa iwo, Kodi mukubwera monga kudzalimbana ndi wachifwamba, potenga malupanga ndi zikwapu podzanditenga Ine? 49Ine ndinali nanu pamodzi tsiku lililonse kuphunzitsa m’kachisi, koma simunandigwire Ine; komatu [zili chomwechi] kuti malemba akwaniritsidwe. 50Ndipo onse anamusiya Iye nathawa. 51Ndipo mnyamata wina anamtsatira Iye ndi chovala cha bafuta atafundika [thupi] lake la maliseche; ndipo [anyamata] anamgwira iye; 52koma iye posiya chovala chake cha bafuta m’mbuyo [mwake], anawathawira iwo ali wamaliseche.

53Ndipo iwo anamtengera Yesu kwa mkulu wa ansembe. Ndipo kumeneko anasonkhana pamodzi akulu ansembe onse ndi akulu ndi alembi. 54Ndipo Petro anamtsatira Iye chapatali, kufikira [iye anali] pakati pa bwalo la nyumba ya chifumu ya mkulu wa ansembe; ndipo anakhala pamodzi ndi anyamata akudzitenthetsa yekha m’kuwala [kwa moto].

55Ndipo ansembe akulu pamodzi ndi akuluakulu a milandu anafuna umboni wakumtsutsa Yesu kuti aphedwe, ndipo sanapeze umboni [uliwonse]. 56Pakuti ambiri anamchitira umboni wabodza womtsutsa Iye, ndipo umboni wawo sunagwirizane. 57Ndipo anthu ena anauka ndi kuperekera umboni womtsutsa Iye, nanena, 58Ife tinamumva Iye akunena, Ine ndidzapasula kachisi uyu amene anamangidwa ndi manja, ndipo pakutha pa masiku atatu ndidzamanga wina osati womangidwa ndi manja. 59Ndiponso amenewa umboni wawo sunagwirizane. 60Ndipo mkulu wa ansembe, pakuimilira pamaso pa onse, anamfunsa Yesu, nanena, Sukuyankha kanthu kodi? Ndi chiyani ichi chimene akukuchitira umboni wotsutsana ndi Iwe? 61Koma Iye anakhala chete, ndipo sanayankhe kanthu. Mkulu wa ansembe anamufunsanso, nati kwa Iye, Kodi ndiwe Khristu, Mwana wa Wodalitsika? 62Ndipo Yesu anati, Ndine amene, ndipo mudzaona Mwana wa munthu atakhala kudzanja lamanja la mphamvu, ndipo akubwera ndi mitambo ya kumwamba. 63Ndipo Mkulu wa ansembe, pong’amba zovala zake, anati, Tifuniranji umboni wina woonjezera? 64Mwazimvera nokha mwano uwu; kodi Iye akuganiza kuti ndi ndani? Ndipo onse anamtsutsa Iye kuti aphedwe. 65Ndipo ena anayamba kumlavulira, ndi kuphimba nkhope yake ndi kum’bwanyula Iye, nanena kwa Iye, Talosera; ndipo asilikali anam’menya makofi ndi manja awo.

66Ndipo Petro pakukhala pansi m’bwalo la milandu la nyumba ya chifumu, anafika m’modzi wa azakazi a mkulu wa ansembe, 67ndipo pakumuona Petro akuotha moto, pomuyang’anitsitsa, anati, Ndipo iwenso unali naye Mnazarene, Yesu. 68Koma iye anakana, nanena, Ine sindikudziwa kapena kumvetsetsa zimene ukunenazi. Ndipo iye anatuluka napita kuchipata; ndipo tambala analira. 69Ndipo mzakaziyu, pakumuona iye, anayambanso kunena kwa iwo amene anaima pamenepo, Uyunso ndi [m’modzi] wa iwo. 70Ndipo iye anakananso. Ndipo pakupitanso kanthawi, iwo amene anaima pafupi anati kwa Petro, Zoonadi ndiwe [m’modzi] wa iwo, pakuti ndiwenso Mgalileya. 71Koma anayamba kutemberera ndi kulumbira, Ine sindimdziwa munthu uyu amene mukunenayu. 72Ndipo kachiwiri tambala analiranso, Ndipo Petro anakumbukira mau amene Yesu analankhula kwa iye, Tambala asanalire kawiri, udzandikana Ine katatu; ndipo pamene iye anaganizira ichi analira.

1Elohimu