Mutu 3
1Ndipo mngelo wa mpingo wa m’Sarde lemba: Zinthu izi anena iye amene ali ndi Mizimu ya Mulung1u isanu ndi iwiri:
ndidziwa ntchito zako, kuti uli nalo dzina lakuti iwe uli ndi moyo, ndipo uli wakufa. 2Khala tcheru, ndipo limbikitsa zinthu zimene zatsala, zimene zatsala pang’ono kufa, pakuti sindinapeze ntchito zako kukhala zokwanira pamaso pa Mulungu2. 3Pamenepo kumbukira m’mene unalandilira ndi kumva, ndi kusunga, ndi kulapa. Ngati pamenepo supenyerera, ndizadza [kwa iwe] ngati wakuba, ndipo suzadziwa nthawi imene ndizadza kwa iwe. 4Koma uli nawo maina ochepa m’Sarde amene sanadetse zovala zawo, ndipo iwo adzayenda ndi ine m’zoyera, chifukwa ali oyenera.
5Iye amene agonjetsa, adzavekedwa zovala zoyera, ndipo sindidzachotsa dzina lake m’buku la moyo, ndipo ndidzavomereza dzina lake pamaso pa Atate ndi pa angelo ake.
6Iye amene ali nalo khutu, amve zimene Mzimu anena kwa mipingo.
7Ndipo kwa mngelo wa mpingo m’Filadefiya lemba: Zinthu izi anena woyera, woonadi; amene ali ndi chifungulo cha Davide, iye amene atsegula ndipo palibe amene angatseke, ndipo akatseka palibe amene angatsegule:
8Ndidziwa ntchito zako: taona, ndaikiza pa iwe khomo lotsegula, limene palibe angalitseke, chifukwa uli nazo mphamvu zochepa, ndipo wasunga mau anga, ndipo sunalikane dzina langa. 9Taona, ndawapanga iwo a sunagoge wa Satana amene amanena kuti ali Ayuda, ndipo sali choncho, koma anama; taona, ndidzapangitsa kuti iwo abwere ndipo adzalambira pa mapazi anu, ndipo azadziwa kuti ndakukonda iwe. 10Chifukwa iwe wasunga mau a chipiliro changa, Inenso ndidzakusunga mu nthawi ya kuyesedwa, kumene kufikire onse okhala padziko lapansi, kuwayesa iwo akukhala padziko lapansi. 11Ndidza msanga: gwiritsitsa chimene uli nacho, kuti aliyense asatenge korona wako.
12Iye amene agonjetsa, ndidzampanga kukhala mzati m’nyumba ya Mulungu3 wanga, ndipo iye sadzatulukanso kunja; ndipo ndidzalemba pa iye dzina la Mulungu4 wanga, ndi dzina la mzinda wa Mulungu5 wanga, Yerusalemu watsopano, umene utsika kuchokera kumwamba, kuchokera kwa Mulungu6 wanga, ndi dzina langa latsopano.
13Iye amene ali nalo khutu, amve zimene Mzimu anena kwa mipingo.
14Ndipo kwa mngelo wa ku mpingo m’Laodikaya lemba: Zinthu izi anena Amenyo, mboni yokhulupirika ndi yoona, chiyambi cha chilengedwe cha Mulungu7:
15Ndidziwa ntchito zako, kuti suli wozizira kapena wotentha; bwenzi utakhala wozizira kapena wotentha. 16Choncho chifukwa iwe uli wofunda, ndipo suli wozizira kapena wotentha, ndidzakulavula mkamwa mwanga. 17Chifukwa iwe umati, ndine wolemera, ndipo ndakula ndili wolemera, ndipo sindinasoweko kanthu, ndipo sudziwa kuti ndiwe osautsika ndi omvetsa chisoni, ndi wosauka, ndi wakhungu, ndi wamaliseche; 18Ine ndikulangiza iwe ugule kwa ine golide woyengeka pamoto, kuti ukhale wolemera; ndi zovala zoyera, kuti uvekedwe, ndi kuti manyazi a umaliseche wako asaonekere; ndi mankhwala a maso upake m’maso mwako, kuti ukathe kupenya. 19Ine ndiwadzudzula ndi kuwalanga onse amene ndiwakonda; chita changu pamenepo ndi kulapa. 20Taona, ndaima pakhomo ndipo ndigogoda; ngati wina amva mau anga ndi kutsekula chitseko, ndidzalowa mwa iye ndi kudya ndi iye, ndi iye ndi ine.
21Iye amene agonjetsa, kwa iye ndidzampatsa kukhala ndi ine mu ufumu wanga; monganso ndagonjetsa, ndipo ndakhala pansi ndi Atate wanga mu ufumu wake.
223Iye amene ali nalo khutu, amve zimene Mzimu anena kwa mipingo.
<note><nbp>1</nbp>Elohimu<nbp>2</nbp>Elohimu<nbp>3</nbp>Elohimu<nbp>4</nbp>Elohimu<nbp>5</nbp>Elohimu<nbp>6</nbp>Elohimu<nbp>7</nbp>Elohimu</note>