Mutu 10

1Abale, kukondwera kwa mtima wanga ndi pemphero langa limene [ndimapereka] kwa Mulungu1 chifukwa cha iwo ndilo chipulumutso. 2Pakuti ine ndiwachitira iwo umboni kuti ali nacho changu pa Mulungu2, koma osati monga mwa chidziwitso. 3Pakuti iwo, pokhala mbuli pa kulungama kwa Mulungu3, ndi kufunafuna kukhazikitsa [kulungama] kwaokwao, sanadzipereke ku kulungama kwa Mulungu4. 4Pakuti Khristu ndiye mathero a lamulo la kulungama kwa aliyense amene akhulupilira.

5Pakuti Mose analemba za kulungama kumene kuli kwa lamulo, munthu amene adzachita zinthu zimenezi adzakhala ndi moyo mwa izo. 6Koma kulungama kwa chikhulupiliro kumayankhula kuti: Musanene mu mtima mwanu, ndani adzakwera kupita kumwamba? ndiko, kutsitsako Khristu; 7kapena, ndani adzatsikira ku dzenje lopanda mathero? ndiko, kukatengako Khristu pakati pa akufa. 8Koma anena chiyani? Mau ali pafupi ndi inu, mkamwa mwanu ndi mumtima mwanu: ndiwo, mau a chikhulupiliro, amene timalalikira: 9kuti ngati uvomereza ndi pakamwa pako Yesu ndi Ambuye, ndi kukhulupilira mu mtima mwako kuti Mulungu5 anamuukitsa pakati pa akufa, udzapulumuka. 10Pakuti ndi mtima ukhulupilira ku kulungama; ndipo ndi mkamwa uvomereza ku chipulumutso. 11Pakuti malemba akuti, Aliyense wokhulupilira pa Iye sadzachita manyazi. 12Pakuti palibe kusiyana pakati pa Myuda ndi Mhelene; pakuti Ambuye yemweyo ali wolemera kwa onse oyitanira pa Iye. 13Pakuti aliyense woyitanira padzina la Ambuye, adzapulumuka. 14Nanga adzayitanira bwanji pa Iye amene sanamkhulupilire? Ndipo adzakhulupilira bwanji pa Iye amene sanamve za Iye? Ndipo adzamva bwanji popanda wina kuwalalikira? 15ndipo adzalalikira bwanji pokhapokha ngati atumidwa? Molingana ndi m’mene kunalembedwera, Akongolelenji mapazi a iwo olalikira uthenga wabwino wa mtendere, a iwo amene alalikira uthenga wabwino wa zinthu zabwino! 16Koma iwo onse sanamvere uthenga wabwino. Pakuti Yesaya anati, Ambuye, ndani amene wakhulupilira uthenga wathu? 17Chomwecho chikhulupiliro chimabwera ndi uthenga, komatu uthenga wa mau a Mulungu6. 1 18Komatu ndinena, Kodi sanamve? Indetu, zoonadi, liwu lawo lafikira kudziko lonse, ndipo mau awo afalikira kwa onse okhala padziko lapansi. 19Komatu ndinena, Kodi Israyeli sanadziwe? Poyamba, Mose anati, Ndidzawachititsa akhale ndi nsanje ndi mtundu wina: kudzera mu mtundu wopulukira ndidzakukwiyitsani. 20Koma Yesaya ali nako kulimba mtima, ndipo anati, Ndinapezedwa ndi iwo amene samandisaka ine; ndadzionetsera kwa iwo amene samandifunafuna ine. 21Koma kwa Israyeli iye anati, Kwa tsiku lonse ndatambasulira dzanja langa kwa anthu osamvera ndi otsutsa.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu