Mutu 14
1Mtima wanu usavutike; mukhulupilira pa Mulungu1, khulupiliraninso pa Ine. 2M’nyumba mwa Atate wanga alimo malo ambiri; ngati sikunali kotero, ndikanakuuzani: pakuti Ine ndipita kukakukonzerani inu malo; 3ndipo ngati ndipita kukakonzera inu malo, ndidzabweranso ndipo ndidzakulandirani mwa Ine ndekha, kuti kumene Ine ndili mukakhalenso. 4Ndipo inu mukudziwa kumene ndikupita, ndipo mukudziwa njira yake. 5Tomasi anati kwa Iye, Ambuye, sitidziwa kumene inu mukupita, ndipo tizadziwa bwanji njira? 6Yesu anati kwa iye, Ine ndine njira, ndi choonadi, ndi moyo. Palibe amene abwera kwa Atate koma mwa Ine. 7Mukanadziwa Ine, mukanadziwanso Atate wanga, ndipo tsopano mwamudziwa Iye ndipo mwamuona Iye. 8Filipo anati kwa Iye, Ambuye, tionetseni Atate ndipo chitikwanira ife. 9Yesu anati kwa iye, Kodi ndili nayo nthawi yaitali ndi inu, ndipo sunandidziwe Ine, Filipo? Iye amene wandiona Ine waona Atate; ndiye unena bwanji, Tionetseni Atate? 10Sukhulupilira kodi kuti ndili mwa Atate, ndipo kuti Atate ali mwa Ine? Mau amene ndilankhula kwa inu sindilankhula kwa Ine ndekha; koma Atate wakukhala mwa Ine, achita ntchito. 11Khulupilirani Ine kuti ndili mwa Atate ndipo Atate ali mwa Ine; koma ngati sizili choncho, khulupilirani Ine chifukwa cha ntchitozo. 12Zoonadi, zoonadi, ndinena kwa inu, Iye wokhulupilira pa Ine, ntchito zimene tichita adzachitanso iye, ndipo adzachita zoposera izi, chifukwa ndipita kwa Atate. 13Ndipo china chilichonse chimene mufunsa m’dzina langa, chimenecho ndidzachichita, kuti Atate akalemekezedwe mwa Mwana. 14Ngati mufunsa chilichonse m’dzina langa, ndidzachichita chimenecho.
15Ngati mundikonda Ine, sungani malamulo anga. 16Ndipo Ine ndidzapempha Atate, ndipo Iye adzakupatsani Mtonthozi wina, kuti akhale ndi inu nthawi zonse, 17Mzimu wa choonadi, amene dziko lapansi sangamulandire, chifukwa sakumuona Iye kapena kumudziwa Iye; koma inu mumdziwa Iye, pakuti akhala ndi inu, ndipo adzakhala mwa inu. 18Sindidzakusiyani inu amasiye, ndikubwera kwa inu. 19Komabe mu kanthawi ndipo dziko lapansi silidzandionanso; koma inu mundiona Ine. 20Tsiku limenelo muzadziwa kuti Ine ndili mwa Atate wanga, ndipo inu mwa Ine, ndipo Ine mwa inu. 21Iye amene ali nawo malamulo anga ndi kuwasunga, ameneyu ndi amene andikonda Ine; koma iye amene andikonda Ine adzakondedwa ndi Atate wanga, ndipo Ine ndidzamkonda iye ndipo ndidzazionetsera ndekha kwa iye. 22Yudase, osati Iskariote, anati kwa Iye, Ambuye, Zitheka bwanji kuti mudzazionetsera nokha kwa ife osati ku dziko lapansi? 23Yesu anayankha nati kwa iye, Ngati wina aliyense akonda Ine, adzasunga mau anga, ndipo Atate wanga adzamkonda iye, ndipo adzabwera kwa iye ndipo tidzapanga kwa Iye mokhalamo mwathu. 24Iye amene sandikonda sasunga mau anga; ndipo mau amene mumamva sianga, koma a Atate amene anandituma Ine. 25Zinthu izi ndalankhula kwa inu, pokhala ndi inu; 26koma Mtonthozi, Mzimu Woyera, amene Atate adzamtuma m’dzina langa, adzakuphunzitsani zinthu zonse, ndipo adzakukumbutsani zinthu zonse zimene ndanena kwa inu. 27Ndikusiyirani inu mtendere; Ndipereka mtendere wanga kwa inu: simonga dziko lapansi likupatsani inu. Mtima wanu usavutike, kapena kuchita mantha. 28Mwamva kuti ndanena kwa inu, ndipita ndipo ndidzabwera kwa inu. Ngati mundikonda Ine mukanakondwera kuti Ine ndipita kwa Atate, pakuti Atate wanga ali wamkulu kuposa Ine. 29Ndipo tsopano ndakuuzani inu zisanachitike, kuti pamene zidzachitika mukakhulupilire. 30Sindidzalankhulanso zambiri ndi inu, pakuti olamulira wa dziko lapansi akubwera, ndipo mwa Ine alibe kanthu; 31koma kuti dziko lapansi likadziwe kuti ndikonda Atate, ndipo monga Atate anandilamulira Ine, ndichitanso chomwecho. Nyamukani, tiyeni tidzipita kuchoka kuno.
1Elohimu