Mutu 9
1Ndipo Iye anati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, alipo ena mwa inu akuima pano amene sadzalawa imfa kufikira adzaona ufumu wa Mulungu1 ukubwera mu mphamvu.
2Ndipo atatha masiku asanu ndi limodzi Yesu anadzitengera kwa [Iye] Petro ndi Yakobo ndi Yohane, ndipo anawatengera iwo pamwamba paphiri padera paokha. Ndipo Iye anasandulika pamaso pawo: 3Ndipo zovala zake zinawala, kuyera kwambiri [monga matalala], kotero kuti wotsuka nsalu wadziko lapansi sangathe kudziyeretsa [izo]. 4Ndipo anaonekera kwa iwo Eliya ndi Mose, ndipo amalankhulana ndi Yesu. 5Ndipo Petro anati pomuyankha Yesu, Rabi, ndi kwabwino kuti ife tili pano; ndipo tiloleni ife timange misasa itatu, wa inu umodzi, ndi wa Mose umodzi, ndi wa Eliya umodzi. 6Pakuti iye sanadziwe kuti anena chiyani, pakuti iwo anazazidwa ndi mantha. 7Ndipo unadza mtambo nuwaphimba iwo, ndipo anamveka mau kuchokera mu mtambo, Uyu ndi Mwana wanga wokondedwa: mvereni Iye. 8Ndipo mwadzidzidzi pounguza, sanaonenso munthu wina aliyense, koma Yesu yekha ali ndi iwo eni.
9Ndipo pamene amasika kuchoka kuphiri, Iye anawalamulira iwo kuti asauze munthu zimene awona, pokhapokha pamene Mwana wa munthu adzauka pakati pa akufa. 10Ndipo iwo anasunga mauwo, nafunsana pakati pawo, Kodi kuuka pakati pa akufa ndi chiyani. 11Ndipo iwo anamfunsa Iye nanena, Chifukwa chiyani alembi amati kuti Eliya adzayamba kubwera? 12Ndipo Iye poyankha anati kwa iwo, Zoonadi Eliya adzayamba kubwera, kudzabwenzeretsa zinthu zonse; ndipo m’mene zinalembedwera za Mwana wa munthu kuti azamva zowawa zambiri ndi kuyesedwa chabe: 13koma Ine ndinena kwa inu kuti Eliya anafikanso, ndipo iwo anapanga kwa iye kalikonse kamene akanatha kupanga, monga momwe zinalembedwa za iye.
14Ndipo pamene Iye anabwera kwa ophunzira ake anaona khamu lalikulu litawazungulira iwo, ndipo alembi amafunsana nawo. 15Ndipo pomwepo khamu lonselo pomuona Iye anali odabwa, ndipo anathamanga kwa [Iye] namlonjera. 16Ndipo Iye anawafunsa iwo, Kodi mumafunsana nawo chiyani? 17Ndipo m’modzi wa mukhamulo anamuyankha Iye, Mphunzitsi, ndinabweretsa kwa Inu mwana wanga, amene ali ndi mzimu wosalankhula; 18ndipo pamene wamugwira iye umamung’amba, ndipo amachita thovu ndi kukukuta mano ake, ndi kunyololoka. Ndipo ine ndinalankhula ndi ophunzira anu, kuti iwo autulutse, ndipo sanakwanitse. 19Koma Iye powayankha iwo anati, M’badwo wosakhulupilira inu? Kodi ndidzapilira nanu kufikira liti? M’bweretseni kwa Ine. 20Ndipo iwo anamubweretsa kwa Iye. Ndipo pakumuona Iye mzimuwo unamng’amba iye nthawi yomweyo; ndipo pakugwa pansi iye anazigudumuza akutuluka thovu. 21Ndipo Iye anawafunsa atate wake, Wakhala ali chonchi nthawi yotalika bwanji? Ndipo Iye anati, Kuyambira ali mwana; 22ndipo kawirikawiri umamuponya pa moto ndi m’madzi kuti ukamuwononge iye: koma ngati mukhoza [kuchita] kanthu kalikonse, tichitereni ife chifundo, ndipo mutithandize. 23Ndipo Yesu anati kwa iye, ‘Ngati mukhoza’ ndiko kuti [ngati ukhoza] kukhulupilira: zinthu zonse zitheka kwa iye wakukhulupilira. 24Ndipo pomwepo atate wa mwanayo anafuula nati [ndi misozi], Ine ndikhulupilira, thandizani kusakhulupilira kwanga. 25Koma Yesu, pakuona kuti khamulo likuthamangira pamodzi, anadzudzula mzimu woipawo, nanena kwa iye, Iwe mzimu wosalankhula ndi wogontha, ndikukulamula, tuluka mwa iye, ndipo usadzalowenso mwa iye. 26Ndipo unafuula ndi kumng’amba [iye] kwambiri, nutuluka; ndipo iye anakhala ngati wamwalira, kotero kuti ambiri anati, wamwalira uyu. 27Koma Yesu, pomugwira padzanja, anamudzutsa, ndipo iye anauka.
28Ndipo pamene Iye analowa m’nyumba, ophunzira ake anamufunsa mseri, Chifukwa chiyani ife sitinakwanitse kutulutsa? 29Ndipo anati kwa iwo, Mtundu uwu sungatuluke wamba komatu ndi pemphero ndi kusala kudya.
30Ndipo pakuchoka apo iwo anapita mopyola Galileya; ndipo Iye sanafune kuti aliyense adziwe ichi; 31pakuti anaphunzitsa ophunzira ake nanena nawo, Mwana wa munthu adzaperekedwa m’manja mwa anthu, ndipo iwo adzamupha Iye; ndipo akadzamupha, pakutha pa masiku atatu Iye adzaukanso, pakutha pa masiku atatu adzaukanso. 32Koma iwo sanazindikire za kulankhulaku, ndipo anaopa kumufunsa Iye.
33Ndipo Iye anafika ku Kapernao, ndipo pakukhala m’nyumba, Iye anawafunsa iwo, Kodi mumatsutsana chiyani panjira? 34Ndipo iwo sanayankhe kanthu, pakuti panjira iwo amatsutsana kuti ndi ndani [amene] anali wamkulu. 35Ndipo pakukhala pansi anaitana khumi ndi awiriwo; ndipo Iye anati kwa iwo, Ngati wina akufuna kukhala woyamba, akhale womaliza wa onse, ndi mtumiki wa onse. 36Ndipo anatenga mwana wamng’ono namuika pakati pawo, ndipo pamene anamfungatira anati kwa iwo, 37Aliyense wakulandira ana otere m’dzina langa, alandira Ine; ndipo aliyense wakulandira Ine, salandira Ine, koma Iye amene anandituma Ine. 38Ndipo Yohane anamuyankha Iye nati, Mphunzitsi, tinaona munthu wina akutulutsa ziwanda m’dzina lanu, amene siwotsatira ife, ndipo ife tinamuletsa, chifukwa iyeyu siwotsatira ife. 39Koma Yesu anati, Musamukanize iye; pakuti palibe amene akhoza kuchita zozizwa m’dzina langa, ndipo [pambuyo] pake ndi kulankhula zoipa za Ine; 40pakuti iye amene salimbana ndi ife ali mbali yathu. 41Komatu aliyense amene adzakupatsani inu madzi kuti mumwe m’dzina [langa], chifukwa ndinu a Khristu, Indetu ndinena kwa inu, ameneyu sadzataya mphoto yake. 42Ndipo aliyense amene adzakhala chokhumudwitsa cha ana awa amene akhulupilira [mwa Ine], kukanakhala bwino kwa iye kuti mwala wa mphero umangidwe pakhosi pake, ndi kuponyedwa m’nyanja. 43Ndipo ngati dzanja lako likhala chokhumudwitsa kwa iwe, lidule: kuli bwino kwa iwe kukalowa m’moyo uli wodulidwa dzanja, kusiyana kukhala ndi manja awiri ndi kupita ku gehena, m’moto wosazimitsika; 44[kumene mphusi zawo sizifa ayi, ndipo moto wake suzimitsika]. 45Ndipo ngati phazi lako likhala chokhumudwitsa kwa iwe, lidule: kuli bwino kwa iwe kukalowa m’moyo wolumala, kusiyana kukhala ndi mapazi awiri ndi kuponyedwa ku gehena, m’moto wosazimitsika; 46[kumene mphusi zawo sizifa ayi, ndipo moto wake suzimitsika]. 47Ndipo ngati diso lako likhala chokhumudwitsa kwa iwe, likolowole: ndi kwabwino kwa iwe kulowa mu ufumu wa Mulungu2 ndi diso limodzi, kusiyana ndi kukhala ndi maso awiri ndi kuponyedwa mu gehena wa moto, 48[kumene mphusi zawo sizifa ayi, ndipo moto wake suzimitsika] 49Pakuti aliyense adzathiridwa mchere wa moto, ndipo nsembe iliyonse idzathiridwa mchere. 50Mchere [ndi] wabwino, koma ngati mchere usukuluka, kodi mudzaukoleretsa ndi chiyani? Khalani ndi mchere mwa inu nokha, ndipo khalani pa mtendere wina ndi mzake.
1Elohimu2Elohimu