Mutu 5
1Aliyense amene amakhulupilira kuti Yesu ndi Khristu anabadwa mwa Mulungu1; ndipo aliyense amene amkonda iye amene anamubala amkondanso amene anabadwa mwa iye. 2Umo tidziwa kuti ife tikonda ana a Mulungu2, pamene tikonda Mulungu3 ndi kusunga malamulo ake. 3Pakuti chimenechi ndicho chikondi cha Mulungu4, kuti tisunga malamulo ake; ndipo malamulo ake sali olemetsa. 4Pakuti chilichonse chobadwa mwa Mulungu5 chimalilaka dziko lapansi; ndipo chimenechi ndicho chipambano chimene chapeza chipambano china padziko lapansi, ndicho chikhulupiliro chathu. 5Ndani amene wapeza chipambano padziko lapansi, komatu iye amene akhulupilira kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu6?
6Ameneyu ndi uja anabwera mwa madzi ndi mwazi, Yesu Khristu; osati mwa madzi okha, koma mwa madzi ndi mwazi. Ndipo ndi Mzimu amene atichitira umboni, pakuti Mzimu ndiye choonadi. 7Pakuti iwo amene achitira umboni alipo atatu: 8Mzimu, ndi madzi, ndi mwazi; ndipo zitatu izi zivomerezana pamodzi. 9Ngati tilandira umboni wa anthu, umboni wa Mulungu7 ndi woposa. Pakuti uwu ndiwo umboni wa Mulungu8 [umene] watichitira okhudza Mwana wake. 10Iye amene akhulupilira pa Mwana wa Mulungu9 ali nawo umboni mwa iye yekha; iye amene sakhulupilira Mulungu10 wamuyesa iye kukhala wabodza, chifukwa sanakhulupilire mu umboni umene Mulungu11 wamchitira okhudza Mwana wake. 11Ndipo umenewu ndiwo umboni, kuti Mulungu12 wapereka kwa ife moyo wosatha; ndipo moyo umenewu uli mwa Mwana wake. 12Iye amene ali naye Mwana ali nawo moyo: iye amene alibe Mwana wa Mulungu13 alibe moyo.
13Zinthu zimenezi ndakulemberani kuti mukadziwe kuti muli nawo moyo wosatha amene mukhulupilira pa Mwana wa Mulungu14.
14Ndipo kumeneku ndiko kulimba mtima kumene tili nako pa iye, kuti ngati tipempha kalikonse molingana ndi chifuniro chake adzatimva. 15Ndipo ngati tidziwa kuti iye amatimva, chilichonse chimene tingapemphe, tidziwa kuti tili nazo zopempha zimene tapempha kwa iye.
16Ngati wina awona m’bale wake akuchimwa tchimo osati lotengera ku imfa, apemphere iye, ndipo adzampatsa moyo, pakuti iwowa ndi amene sanachimwa kufikira imfa. Pali tchimo la kuimfa: sindinena lotere kuti mupemphere. 17Chosalungama chilichonse ndicho tchimo; ndipo lilipo tchimo losatengera ku imfa. 18Ife tidziwa kuti aliyense wobadwa mwa Mulungu15 samachimwa, koma iye amene anabadwa mwa Mulungu16 amazisunga yekha, ndipo woipayo samamkhudza iye. 19Tidziwa ife kuti tili a Mulungu17, ndipo dziko lonse lapansi likhala mwa woipayo. 20Ndipo tidziwa kuti Mwana wa Mulungu18 wafika, ndipo watipatsa ife kumvetsetsa kuti timdziwe iye amene ali woonayo; ndipo ife tili mwa iye amene ali woonayo, mwa Mwana wake Yesu Khristu. Iye ndiye Mulungu19 woonayo ndiponso moyo wosatha.
21 Ana inu, zisungireni nokha kupewa mafano.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu7Elohimu8Elohimu9Elohimu10Elohimu11Elohimu12Elohimu13Elohimu14Elohimu15Elohimu16Elohimu17Elohimu18Elohimu19Elohimu