Mutu 1
1Pachiyambi panali Mau, ndipo Mau anali ndi Mulungu1, ndipo Mauwo anali Mulungu2. 2Iye anali pachiyambi ndi Mulungu3. 3Zinthu zonse zinalandiridwa mwa iye, ndipo popanda iye palibe kanthu [kalikonse] kamene kakanalandiridwa. 4Mwa iye munali moyo, ndipo moyowo kunali kuwala kwa anthu. 5Ndipo kuwala kunaonekera mu mdima, ndipo mdima sunakuzindikire ayi.
6Panali munthu wotumidwa kuchokera kwa Mulungu4, dzina lake Yohane. 7Iye anabwera kudzachitira umboni, kuti achitire umboni zokhudza kuunika, kuti onse akakhulupilire mwa iye. 8Iye sanali kuunikako, koma kuti akachitire umboni zokhudza kuunika. 9Kuunika kwenikweni kunali kwakuti, pakudza m’dziko lapansi, kukaunikire munthu wina aliyense. 10Iye anali m’dziko lapansi, ndi dziko lapansi linali naye, ndipo dziko lapansi silinamzindikire Iye. 11Iye anabwera kwa zake zomwe, ndipo zake zomwe sizinamlandire Iye; 12koma onse amene anamlandira Iye, kwa iwo anawapatsa ufulu okhala ana a Mulungu5, kwa iwo akukhulupilira dzina lake; 13amene sanabadwe, mwa mwazi, kapena chifuniro cha thupi, kapenanso chifuniro cha munthu, koma cha Mulungu6.
14Ndipo Mau anasandulika thupi, ndipo anakhala pakati pathu (ndipo tinaona ulemelero wake, ulemelero wonga wa wobadwa yekha wa Atate), wodzala ndi chisomo ndiponso choonadi; 15 (Yohane akuchitira umboni za Iye, ndipo anafuula, nati, Uyu ndi amene ndinanena za Iye, wakudza pambuyo panga ali wofunika kuposa ine, pakuti analipo kale ine ndisanabadwe;) 16pakuti mwakudzala kwake tonsefe talandira, ndi chisomo pamwamba pa chisomo. 17Pakuti chilamulo chinaperekedwa ndi Mose: chisomo ndi choonadi zinadza mwa Yesu Khristu. 18Palibe anaona Mulungu7 nthawi ina iliyonse; Mwana wake yekhayo, amene ali pachifuwa cha Atate, anamfotokozera [Iye].
19Ndipo umenewu ndiwo umboni wa Yohane, pamene Ayuda anatuma kuchokera ku Yerusalemu ansembe ndi Alevi kuti adzamufunse iye, Ndiwe ndani? 20Ndipo iye anavomera sanakane, navomereza, Sindine Khristu. 21Ndipo iwo anamufunsa iye, Nanga bwanji? Kodi ndiwe Eliya? Ndipo iye anati, Sindine ayi. Kodi ndiwe mneneri? Ndipo iye anayankha, Ayi. 22Kotero iwo anati kwa iye, Ndiwe ndani? Kuti tikapereke yankho kwa iwo amene atituma. Unena chiyani za iwe wekha? 23Iye anati, Ndine mau wofuula m’chipululu, ongolani njira ya Ambuye, monga ananenera Yesaya mneneri. 24Ndipo iwo anatumidwa pakati pa Afarisi. 25Ndipo iwo anamufunsa nati kwa iye, Chifukwa chiyani nanga ukubatiza, ngati sindiwe Khristu, kapena Eliya, kapenanso mneneri? 26Yohane anawayankha iwo nati, Ine ndibatiza ndi madzi. Pakati panu paima wina, amene simukumudziwa, 27amene akudza pambuyo panga, zingwe za nkhwayira yake sindili woyenera kumasula. 28Zinthu zimenezi zinachitika m’Betaniya, kutsidya kwa Yordano, kumene Yohane amabatiza.
29M’mawa mwake anaona Yesu akubwera kwa iye, ndipo anati, Taonani Mwanawankhosa wa Mulungu8, amene amachotsa tchimo la dziko lapansi. 30Iyeyu ndi amene ine ndinanena, Munthu wakudza pambuyo panga amene adzatenga malo anga, chifukwa Iye analiko ine ndisanabadwe; 31ndipo ine sindinamdziwe; koma kuti akaonetsedwe kwa Israyeli, kotero ndadza ine kubatiza ndi madzi.
32Ndipo Yohane anachitira umboni, nati, Ndinaona Mzimu akutsika ngati nkhunda kuchokera kumwamba, ndipo unakhala pa Iye. 33Ndipo ine sindinamzindikire Iye; koma Iye amene anandituma ine kubatiza ndi madzi, anati kwa ine, Pa Iye amene udzaona Mzimu akutsikira ndi kukhala pa Iye, ameneyo ndi amene abatiza ndi Mzimu Woyera. 34Ndipo ndaona ndi kuchitira umboni kuti ameneyu ndi Mwana wa Mulungu9.
35M’mawa mwakenso, anayimilira Yohane pamodzi ndi ophunzira ake awiri. 36Ndipo pomuona Yesu akuyenda, iye anati, Taonani Mwanawankhosa wa Mulungu10. 37Ndipo ophunzira awiri aja anamumva iye akulankhula, ndipo anamtsata Yesu. 38Koma Yesu potembenuka, ndi kuona iwo akumtsatira, anati kwa iwo, Mukufuna chiyani? Ndipo iwo anati kwa iye, Rabi (zimene, potanthauzira, zisonyeza Mphunzitsi), kodi mumakhala kuti? 39Iye anati kwa iwo, Bwerani mudzaone. Pamenepo iwo anapita, ndipo anaona kumene amakhala; ndipo iwo anakhala naye tsiku limenelo. Ndipo linali ngati ola lakhumi. 40Andreya, m’bale wake wa Simoni Petro, anali m’modzi wa awiri amene anamva [izi] kwa Yohane namtsata Iye. 41Poyamba iye anampeza m’bale wake Simoni, ndipo anati kwa iye, Tampeza Mesiya (ndiko kutanthauza Khristu). 42Ndipo anamtsogolera iye kwa Yesu. Yesu pakumuona iye anati, Ndiwe Simoni, mwana wa Yonasi; udzatchedwa Kefa (ndiko kutanthauza mwala).
43M’mawa wake anafuna kutuluka kunka ku Galileya, ndipo Yesu anampeza Filipo, nati kwa iye, nditsate Ine. 44Ndipo Filipo anali wochokera ku Betsaida, wa mzinda wa Andreya ndi Petro. 45Filipo anampeza Natanayeli, ndipo anati kwa iye, Tampeza Iye amene Mose analemba m’chilamulo, ndi aneneri, Yesu, mwana wa Yosefe, amene ali waku Nazareti. 46Ndipo Natanayeli anati kwa iye, Kodi kanthu kabwino kakhoza kutuluka mu Nazareti? Filipo anati kwa iye, Bwera udzaone. 47Yesu anamuona Natanayeli akubwera kwa Iye, ndipo anati kwa iye, Taonani [munthu] m’Israyeli weniweni, amene mwa iye mulibe chinyengo. 48Natanayeli anati kwa Iye, Munandidziwira kuti? Yesu anati kwa iye, Filipo asanakuitane iwe, pamene unali pansi pa mtengo wa mkuyu, ndinakuona iwe. 49Natanayeli anayankha nati kwa Iye, Rabi, ndinu Mwana wa Mulungu11, ndinu Mfumu ya Israyeli. 50Yesu anayankha nati kwa iye, Chifukwa ndinati kwa iwe, ndinakuona uli pansi pa mtengo wa mkuyu, wakhulupilira kodi? Udzaona zinthu zazikulu kuposera izi. 51Ndipo anati kwa iye, Zoonadi, zoonadi ndinena kwa inu, pamenepo mudzaona kumwamba kutatseguka, ndipo angelo a Mulungu12 akukwera ndi kutsika pa Mwana wa munthu.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu7Elohimu8Elohimu9Elohimu10Elohimu11Elohimu12Elohimu