Mutu 22
1Tsopano phwando la mkate wopanda chotupitsa, limene limatchedwa paska, linawandikira, 2ndipo ansembe ndi alembi anafuna momwe angamuphere Iye; pakuti iwo anaopa anthu.
3Ndipo Satana analowa mwa Yudase, amene anatchulidwanso Isikariote, pokhala m’modzi wa khumi ndi awiriwo. 4Ndipo iye anapita nalankhula ndi ansembe akulu ndi akazembe m’mene angamuperekere Iye kwa iwo. 5Ndipo iwo anakondwera, nagwirizana kumupatsa Iye ndalama. 6Ndipo iye anagwirizana nawo kuchita ichi, nafunafuna mpata wabwino wakumperekera kwa iwo kumchotsa Iye ku khamulo.
7Ndipo tsiku la mkate wopanda chotupitsa linafika, limene nsembe ya paska inayenera kuphedwa. 8Ndipo Iye anatuma Petro ndi Yohane, nanena, Pitani ndi kukakonza paska kwa ife, kuti tidye imeneyo. 9Koma iwo anati kwa Iye, Kodi tikakonzere kuti [iyo]? 10Ndipo Iye anati kwa iwo, Taonani, pamene mudzalowa mu mzinda mudzakumana naye munthu, wakunyamula mtsuko wa madzi; mtsatireni mnyumba imene iye adzalowa; 11ndipo mukanene ndi mwini nyumba, Mphunzitsi anena kwa iwe, chipinda cha alendo chili kuti m’mene ndidzadyera paska ndi ophunzira anga? 12Ndipo iye akakuonetsani chipinda chachikulu chapamwamba chokonzeka: m’menemo kandikonzereni. 13Ndipo atapita iwo anapeza monga Iye ananenera kwa iwo; ndipo iwo anakonza paska.
14Ndipo pamene ola linafika, Iye anakhala pa gome, pamodzi ndi ophunzira [khumi ndi awiriwo]. 15Ndipo Iye anati kwa iwo, Ndi chikhumbokhumbo ndakhala ndikufunitsitsa kudya paska uyu pamodzi ndi inu ndisanamve zowawa. 16Pakuti Ine ndinena kwa inu, kuti sindizadyanso konse uyu kufikira udzakwaniritsidwa mu ufumu wa Mulungu1. 17Ndipo atalandira chikho, pamene anayamika anati, Tengani ichi ndipo mugawane pakati panu. 18Pakuti ndinena kwa inu, Kuti sindidzamwanso konse chipatso cha mpesa kufikira ufumu wa Mulungu2 ukadza. 19Ndipo pakutenga mkate, pamene anayamika, anaunyema [iwo], naupereka kwa iwo, nanena, Limeneli ndi thupi langa limene lapatsidwa kwa inu: chitani izi pokumbukira Ine. 20Chimodzimodzinso chikho, atatha mgonero Iye anati, Chikho ichi [ndilo] pangano latsopano m’mwazi wanga, umene unakhetsedwa chifukwa cha inu. 21Komabe, onani, dzanja la iye wondipereka [ali] ndi Ine pagome pano; 22ndipo Mwana wa munthu apita monga kunaikidwiratu, koma tsoka kwa munthu amene adzampereka Iye. 23Ndipo iwo anayamba kufunsana pakati pawo kuti ndani amene adzachita ichi.
24Ndipo panalinso kulimbana pakati pawo kuti ndani mwa iwo amene anali wamkulu. 25Ndipo Iye anati kwa iwo, Mafumu amitundu amawalamulira iwo, ndipo amene amaonetsera ulamuliro pa iwo amatchedwa athandizi. 26Koma ndi inu sizidzakhala choncho; koma lolani wamkulu pakati panu akhale ngati wamng’ono, ndipo mtsogoleri ngati wotumikira. 27Pakuti ndi uti amene ali wamkulu, iye amene akudya pagome kapena amene akutumikira? Kodi si uyo amene akudya pagome? Koma Ine ndili pakati panu ngati wotumikira. 28Komatu inu muli amene mwapilira nane m’mayesero anga. 29Ndipo Ine ndakusankhirani inu, monga Atate wanga anandisankhira Ine ufumu, 30kuti mukadye ndi kumwa pagome langa mu ufumu wanga, ndi kukhala pagome langa mu ufumu wanga, ndi kukhala pa mpando wa ulamuliro kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israyeli.
31Ndipo Ambuye anati, Simoni, Simoni, taona Satana wafunitsitsa kukutenga, akupete [iwe] ngati tirigu; 32koma Ine ndakupempherera iwe kuti chikhulupiliro chako chisalephere; ndipo iwe, pamene wabwenzeretsedwa, ukawatsimikizire abale ako. 33Ndipo iye anati, Ambuye, ndi inu ndili wokonzeka kupita kundende ngakhale kufa kumene. 34Ndipo Iye anati, Ndikuuza Petro, tambala sadzalira lero usanandikane katatu kuti sundidziwa Ine.
35Ndipo Iye anati kwa iwo, Pamene ndinakutumani opanda chikwama cha ndalama ndi thumba la chakudya ndi nkhwaila, kodi munasowa kanthu? Ndipo iwo anati sitinasowe kanthu. 36Pamenepo Iye anati kwa iwo, Koma tsopano iye amene ali nacho chikwama cha ndalama atenge, chimodzimodzinso amene ali nalo thumba la chakudya atengenso, ndipo amene alibe agulitse chofunda chake ndi kugula lupanga; 37pakuti ndinena kwa inu, kuti ichi chimene chinalembedwa chikakwaniritsidwe mwa Ine, Ndipo anawerengedwa pamodzi ndi anthu osatsata lamulo: pakutinso zinthu zokhudza Ine zili ndi pothera. 38Ndipo iwo anati, Ambuye, taonani tili nawo malupanga awiri. Ndipo Iye anati kwa iwo, Zakwanira.
39Ndipo anapita Iye molingana ndi chikhalidwe ku phiri la Azitona, ndipo ophunzira anamutsatira Iye. 40Ndipo pamene Iye anafika kumaloko anati kwa iwo, Pempherani kuti musalowe m’mayesero. 41Ndipo Iye anadzipatula kwa iwo kutalikana kwake ngati kuponya mwala, ndipo pamene anagwada pansi anapemphera, 42nanena, Atate, ngati nkutheka mundichotsere chikho ichi kwa Ine: — komatu pamenepo, osati chifuniro changa, koma chanu chichitike. 43Ndipo mngelo anaonekera kwa Iye kuchokera kumwamba namlimbikitsa. 44Ndipo pakulimbana mkati mwake anapemphera kolimba. Ndipo thukuta lake linali ngati madontho a magazi, akugwa pansi. 45Ndipo ananyamuka kopemphera, nabwera kwa ophunzira, nawapeza akugona ndi chisoni. 46Ndipo Iye anati kwa iwo, Chifukwa chiyani mukugona? Dzukani ndi kupemphera kuti musalowe m’kuyesedwa.
47Pamene anali chilankhulire, taonani, khamulo, ndi iye wotchedwa Yudase, m’modzi wa khumi ndi awiriyo, akuwatsogolera iwo, ndipo anafika pafupi ndi Yesu nampsopsona. 48Ndipo Yesu anati kwa iye, Kodi ukupereka Mwana wa munthu ndi chipsopsono? 49Ndipo iwo amene anamzungulira Iye poona zimene zidzatsatira, anati [kwa Iye], Ambuye, kodi tiwakanthe iwo ndi lupanga? 50Ndipo wina wa iwo pakati pawo anakantha kapolo wa mkulu wansembe namdula khutu lake lakumanja. 51Ndipo Yesu poyankha anati, Musavutike mpaka chonchi; ndipo anakhudza khutu lake, namchiritsa iye. 52Ndipo Yesu anati kwa ansembe akulu ndi akapitao a kachisi ndi akulu, amene anabwera kudzamugwira, Kodi mwabwera ngati mukudzagwira wachifwamba ndi malupanga komanso zikwapu? 53Pamene Ine tsiku ndi tsiku ndinali ndi inu m’kachisi simunatanse manja anu kufuna kundigwira; koma lino ndi ola lanu ndi mphamvu ya kumidima.
54Ndipo anamgwira Iye, namtsogolera kunyumba ya wamkulu wa nsembe. Ndipo Petro amalondola chapatali. 55Ndipo iwo atakoleza moto pakati pa bwalo anakhala pansi pamodzi, ndipo Petro anakhalanso pakati pawo. 56Ndipo mzakadzi wina, atamuona iye atakhala powala, ndipo anamuyang’anitsitsa iye, nati, [Munthu] uyu anali pamodzi ndi Iye. 57Koma anamkana [Iye], nanena, Mkazi iwe, ine sindikumudziwa ameneyu. 58Ndipo nthawi yochepa wina pakumuona iye anati, Uyu ndi m’modzi wa iwo. Koma Petro anati, Munthu iwe, sindine ayi. 59Ndipo pakutha pa ola limodzi munthu wina anatsimikizira, nanena, Kunena zoona [munthu] uyunso anali ndi Iye, pakuti nayenso ndi m’Galileya. 60Ndipo Petro anati, Munthu iwe, sindikudziwa chimene ukulankhulacho. Ndipo nthawi yomweyo, adakali chilankhulire, tambala analira. 61Ndipo Ambuye, potembenuka, anamuyang’ana Petro; ndipo Petro anakumbukira mau a Ambuye, m’mene analankhulira kwa iye, Tambala asanalire udzandikana Ine katatu. 62Ndipo Petro, anatuluka panja, nalira mowawidwa mtima.
63Ndipo anthu amene anamumva anamnyoza, nam’menya [Iye]; 64ndipo anamuphimba kumaso, namufunsa nanena, Tanenera, ndani amene wakumenya Iwe? 65Ndipo iwo analankhula zinthu zambiri zopweteka kwa Iye.
66Ndipo pamene kunacha, bungwe la akulu a anthu, amene ndi ansembe akulu pamodzi ndi alembi, anasonkhana pamodzi, namtengera Iye ku bwalo lawo, nanena, 67Ngati ndiwe Khristu tiuze ife. Ndipo Iye anati kwa iwo, Ngakhale ndikuuzeni, simungakhulupilire konse; 68ndipo ngati nditakufunsani simungathe kundiyankha konse, kapena kundisiya; 69koma kuyambira tsopano Mwana wa munthu adzakhala padzanja lamanja la mphamvu la Mulungu3. 70Ndipo iwo onse anati, Ndiye kuti ndiwe Mwana wa Mulungu4? Ndipo Iye anati kwa iwo, Mwatero ndi inu kuti ndine amene. 71Ndipo iwo anati, Tifuniranji umboni wina, pakuti tadzimvera tokha zotuluka m’kamwa mwake?
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu