Mutu 18
1Yesu, pamene ananena zinthu izi, anatuluka pamodzi ndi ophunzira ake kunka kutsidya kwa mtsinje wa Kedroni, kumene kunali munda, m’mene Iye analowamo, pamodzi ndi ophunzira ake. 2Ndipo Yudasenso, amene adzampereka Iye, anadziwa malowa, chifukwa Yesu amakonda kupita kumeneko, pamodzi ndi ophunzira ake. 3Pamenepo Yudase, m’mene anatenga gulu, ndi asilikali a akulu ansembe ndi Afarisi, anabwera kumeneko ndi nyali ndi miuni ndi zida. 4Pamenepo Yesu, podziwa zonse zimene zikudza kwa Iye, anapita ndi kunena nawo, Mukufuna ndani? 5Iwo anamuyankha Iye, Yesu Mnazarayo. Yesu anati kwa iwo, Ndine amene. Ndipo Yudasenso, amene anampereka Iye, anaima nawo pamodzi. 6Pamene Iye ananena kwa iwo, Ndine amene, anabwerera m’mbuyo ndipo anagwa pansi. 7Iye anawafunsaso, Mukufuna ndani? Ndipo anati, Yesu Mnazarayo. 8Yesu anayankha, Ndakuuzani kuti Ndine amene: pamenepo ngati mukufuna Ine, aloleni awa apite; 9kuti mau akakwaniritsidwe amene Iye analankhula, iwo amene munandipatsa ndinawasunga, ndipo palibe mwa iwo amene anaonongeka. 10Pamenepo Simoni Petro, pokhala nalo lupanga, analisolola, nagwaza kapolo wa mkulu wa ansembe nadula khutu lake; ndipo dzina la kapoloyo linali Malko. 11Pamenepo Yesu anati kwa Petro, Ika lupanga lako m’chimake; chikho chimene Atate wandipatsa, kodi ndisamwere chimwenechi?
12Pamenepo gululo, ndi mkulu wa asilikali, pamodzi ndi asilikali a Ayuda, anamgwira Yesu namumanga: 13ndipo iwo anapita naye poyamba kwa Anasi; pakuti anali mpongozi wake wa Kayafa, amene anali mkulu wa ansembe chaka chimenecho. 14Komatu anali Kayafa amene anapangira Ayuda kuti kunali kwabwino kuti munthu m’modzi akafe chifukwa cha anthu. 15Tsopano Simoni Petro anatsatira Yesu, ndi wophunzira wina. Koma wophunzira ameneyu anali wodziwika kwa mkulu wa ansembe, ndipo anapita pamodzi ndi Yesu mnyumba ya mkulu wa ansembe; 16koma Petro anayima pakhomo kunja. Pamenepo wophunzira winayo, amene anali wodziwika ndi mkulu wa ansembe, anatuluka nalankhula kwa wapakhomo ndipo anamulowetsa Petro. 17Pamenepo namwali, amene anali wapakhomoyo, anati kwa Petro, Iwenso ndi m’modzi wa ophunzira a munthu uyu? Iye anati, Sindine ayi. 18Koma akapolo ndi asilikali, atakoleza moto wa makala (popeza kumazizira), anayimilira ndi kumaothera motowo; ndipo Petro anayimilira nawo pamodzi ndi kuothera motowo. 19Pamenepo mkulu wa ansembe anamufunsa Yesu zokhudza ophunzira ake komanso chiphunzitso chake. 20Yesu anamuyankha iye, Ine ndinalankhula poyera kudziko lapansi; ndinaphunzitsa nthawi zonse m’masunagoge ndi m’kachisi, kumene Ayuda onse amasonkhana pamodzi, ndipo kumbali palibe chimene ndinalankhula. 21Chifukwa chiyani mukundifunsa Ine? Afunseni amene anamva, zimene ndinalankhula kwa iwo; taonani, iwo akudziwa zimene Ine ndinalankhula. 22Koma pamene Iye amalankhula zinthu izi, m’modzi wa asilikali amene anayimilira pafupi anamenya chibakera ku nkhope kwa Yesu, nati, Iwe ungamuyankhe choncho mkulu wa ansembe? 23Yesu anamuyankha iye, Ngati ndalankhula choipa, uchitire umboni ku choipacho; koma ngati ndalankhula bwino, chifukwa chiyani ukundimenya? 24Pamenepo Anasi anamtumiza Iye womangidwa kwa Kayafa mkulu wa ansembe.
25Koma Simoni Petro anali kuyimilira akuwothera moto. Iwo anati kwa iye, Suli iwenso wa akuphunzira ake? Iye anakana, ndipo anati, Sindine ayi. 26M’modzi wa akapolo a mkulu wa ansembe, m’bale wake wa uja amene Petro anamdula khutu, anati, Kodi sindinakuone iwe m’munda pamodzi ndi Iye? 27Pamenepo Petro anakananso, ndipo nthawi yomweyo tambala analira. 28Anamtsogolera Iye kuchoka kwa Kayafa kupita ku bwalo la milandu; ndipo unali m’bandakucha. Ndipo iwo sanalowe m’bwalo la milandu, kuti asadetsedwe, koma kuti akadye pasaka. 29Pamenepo Pilato anatuluka kwa iwo ndipo anati, Mwabweretsa chomuneneza chanji chotsutsana naye munthu uyu? 30Iwo anayankha ndipo anati kwa Iye, Munthu uyu akanakhala kuti siwoipa, sitikanampereka kwa inu. 31Pamenepo Pilato anati kwa iwo, Mtengeni Iye, ndipo mumuweruza molingana ndi chilamulo chanu. Pamenepo Ayuda anati kwa iye, Sikuloledwa kwa ife kupha munthu wina aliyense; 32kuti mau a Yesu akakwaniritsidwe amene analankhula, kuonetsera imfa imene Iye adzafa. 33Pamenepo Pilato analowanso m’bwalo la milandu ndipo anamuitana Yesu, nati kwa Iye, Kodi ndiwe mfumu ya Ayuda? 34Yesu anamuyankha [iye], Mwanena izi nokha, kapena ena alankhula ichi kwa inu zokhudza Ine? 35Pilato anayankha, Kodi ndine Myuda? Mtundu wako ndi akulu ansembe akupereka Iwe kwa ine: wachita chiyani? 36Yesu anayankha, Ufumu wanga si wadziko lapansili; ufumu wanga ukanakhala wa dziko lapansili, anyamata anga akanamenya nkhondo kuti ndisaperekedwe kwa Ayuda; koma tsopano ufumu wanga siwochokera kuno. 37Pamenepo Pilato anati kwa Iye, Ndiye kuti ndiwe mfumu? Yesu anayankha, Mwanena ichi inuyo, kuti ndine mfumu. Ine ndinabadwa chifukwa cha ichi, ndipo pa chifukwa chimenechi ndabwera padziko lapansi, kuti ndikachitire umboni ku choonadi. Aliyense amene ali wa choonadi amva mau anga. 38Pilato anati kwa Iye, Choonadi ndi chiti? Ndipo atalankhula izi iye anapitanso kwa Ayuda, ndipo anati kwa iwo, Sindikupeza cholakwa chilichonse mwa Iye. 39Komatu muli ndi chikhalidwe kuti ine ndimakumasulirani munthu [wina] pa pasaka; kodi mukufuna ndikumasulireni mfumu ya Ayuda? 40Iwo onse anafuulanso, nanena, Osati [munthu] uyu, koma Baraba. Tsopanotu Baraba anali wachifwamba.