Mutu 10
1Tsopano zitapita izi Ambuye anasankha enanso makumi asanu ndi awiri, ndipo anawatumiza iwo awiriawiri pamaso pake mu mzinda ulionse ndi malo alionse kumene Iye amayenera kubwerako. 2Ndipo Iye anati kwa iwo, Zokolola ndithu ndi zambiri, koma ogwira ntchito ndi ochepa; chotero pempherani Ambuye wa zokolola kuti atumize antchito ake ku kukolola kwake. 3Pitani: taonani Ine nditumiza inu ngati nkhosa pakati pa mimbulu. 4Musatenge chikwama kapena polembapo kapenanso nsapato, ndipo musalonjere munthu wina aliyense panjira. 5Ndipo nyumba ina iliyonse imene mukalowa, choyamba nenani, Mtendere ukhale m’nyumba muno. 6Ndipo ngati mwana wa mtendere ali m’menemo, mtendere wanu ukhale pamenepo; koma ngati mulibe mtenderewo ubwererenso kwa inu. 7Ndipo m’nyumba momwemo khalani, idyani ndi kumwa zinthu zimene iwo ali nazo; pakuti wantchito ayenera mphoto yake. Musamachoke nyumba ndi nyumba. 8Ndipo mzinda ulionse umene mukalowa ndipo akulandirani, idyani chimene chapatsidwa kwa inu, 9ndipo chiritsani odwala m’menemo, ndipo munene kwa iwo, Ufumu wa Mulungu1 wayandikira kwa inu. 10Komatu mzinda uliwonse umene mudzalowa ndipo sakulandirani, pitani m’makwalala mwake ndi kunena, 11Ngakhale fumbi la mu mzinda mwanu, limene lakakamira ku mapazi athu, tilisansira motsutsana ndi inu; koma dziwani ichi, kuti ufumu wa Mulungu2 wayandikira. 12Ine ndinena kwa inu kudzakhala kopepuka kwa Sodomu mu tsiku lija kuposera mzinda umenewo. 13Tsoka kwa iwe, Korazini! Tsoka kwa iwe, Betsaida! Pakuti ngati ntchito za mphamvu zimene zinachitika mwa inu zikadachitikira ku Turo ndi Sidoni, iwo akadalapa kalekale, povala chiguduli ndi kukhala m’mapulusa. 14Komatu kudzakhala kopepuka kwa Turo ndi Sidoni pa chiweruzo kusiyana ndi inu. 15Ndipo iwe, Karpenao, amene wakwezedwa kupita kumwamba, udzatsitsidwanso kufikira ku hade. 16Iye amene amvera inu amvera Ine; ndipo iye wakukana inu akana Ine; ndipo amene akana Ine akana Iye amene anandituma Ine.
17Ndipo makumi asanu ndi awiriwo anabwerera ndi chimwemwe, nanena, Ambuye, ngakhale ziwanda zinatigonjera ife kudzera mu dzina lanu. 18Ndipo Iye anati kwa iwo, Ndinaona Satana ngati mphenzi akugwa kuchokera kumwamba. 19Taonani, ndikupatsani inu mphamvu ya kuponda pa njoka ndi zinkhanira ndi pa mphamvu yonse ya mdani, ndipo palibe chimene chidzapweteka inu. 20Chomwecho musakondwere mu ichi, kuti mizimu inagonjera inu, koma kondwerani kuti maina anu alembedwa m’buku la kumwamba.
21Mu ola lomwelo Yesu anakondwera mu mzimu wake nati, Ndikulemekezani inu, Atate, Ambuye wa kumwamba ndi dziko lapansi, kuti munabisira zinthu izi kwa anzeru ndi ozindikira, ndipo mwazivumbulutsira kwa makanda: inde, Atate, pakuti ichi chinakondweretsa pamaso panu. 22Zinthu zonse zaperekedwa kwa Ine ndi Atate, ndipo palibe amene adziwa kuti Mwana ndi ndani komatu Atate, ndipo Atate ndi ndani komatu Mwana, ndi kwa amene Mwana wasangalatsidwa kuti amuululire. 23Ndipo potembenukira kwa ophunzira kumbali Iye anati, Odala maso amene awona zinthu zimene inu mwaona. 24Pakuti ndinena kwa inu kuti aneneri ambiri ndi mafumu anafunitsitsa kuwona zinthu zimene inu mwaona, komatu sanathe kuziona [izo]; ndi kumva zinthu zimene mwazimva, komatu sanazimve [izo] .
25Ndipo taonani, munthu wina wa za malamulo anayimilira nafuna kumuyesa Iye, nanena, Mphunzitsi, ndichite chiyani, kuti ndikalowe moyo wosatha? 26Ndipo anati kwa iye, Kodi m’malamulo munalembedwa chiyani? Umawerenga bwanji? 27Koma iye poyankha anati, Uzikonda Ambuye Mulungu3 wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu zako zonse, ndi kumvetsetsa kwako konse; ndi kukonda mnasi wako monga uzikondera iwe mwini. 28Ndipo anati kwa iye, Wayankha bwino: kachite zimenezi ndipo udzakhala ndi moyo. 29Koma iye, pokhumba kuzilungamitsa yekha, anati kwa Yesu, Ndipo mnasi wanga ndi uti? 30Ndipo Yesu poyankha anati, Munthu wina amatsika kuchokera ku Yerusalemu kupita ku Yeriko ndipo anagwidwa [m’manja mwa] achifwamba, amenenso, anamvula zovala namsiya ndi mabala, wosala pang’ono kufa. 31Ndipo wansembe wina kunachitika kuti amatsikira njira yomweyo, ndipo pomuona iye, anamulambalala nadutsa mbali ina; 32ndipo chimodzimodzinso Mlevi, anafika pa malopo namuyang’ana [iye] ndipo anadutsanso mbali ina. 33Koma Msamaliya wina ali pa ulendo anafika kwa iye, ndipo pomuona [iye], anagwidwa chifundo, 34ndipo anafika [kwa iye] ndipo anamanga mabala ake, nathirapo mafuta ndi vinyo; ndipo pamene anamuika iye pa bulu wake, anamutengera kunyumba yogona alendo namsamalira iye. 35Ndipo m’mawa mwake [pochoka], anatenga marupiya atheka awiri nampatsa woyang’anira nyumba yogona alendo, ndipo anati kwa iye, Umsamalire, ndipo kalikonse kamene udzagwiritsa ntchito koonjezera, ndidzakubwezera ndikabwera. 36Ndani [tsopano] mwa atatuwa akuoneka kwa iwe kukhala mnasi wa uyu wogwidwa [m’manja mwa] achifwambayu? 37Ndipo iye anati, Uyu amene anamuonetsera chifundoyu. Ndipo Yesu anati kwa iye, Pita ukachite iwe chimodzimodzi.
38Ndipo kunachitika pamene iwo amapita kuti Iye analowa m’mudzi wina; ndipo mkazi wina, dzina lake Marita, anamulandira m’nyumba mwake. 39Ndipo anali ndi m'bale wake wotchedwa Mariya, amenenso, pokhala pa mapazi a Yesu anamvera mau ake. 40Tsopano Marita anatanganidwa ndi kutumikira, ndipo anabwera kwa Iye nati, Ambuye, kodi simusamala kuti m’bale wanga wandisiyira ndekha kutumikira? Tamulankhulani kuti andithandize ine. 41Koma Yesu poyankha anati kwa iye, Marita, Marita, iwe ukusamalira ndi kuvutika ndi zinthu zambiri; 42koma chisoweka chinthu chimodzi, ndipo Mariya wasankha mbali yabwinoyo, imene singachotsedwe kwa iye.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu