Mutu 7

1Pamenepo pokhala nawo malonjezano awa, wokondeka, tiyeni tidziyeretse tokha ku zodetsa zonse za thupi ndi mzimu, kukonzanso chiyero m’kuopa 1Mulungu.

2Tilandireni: ife sitinapsinje munthu wina aliyense, sitinasokoneze munthu wina aliyense, sitinachitire phindu pa munthu wina aliyense. 3Sindikulankhula kuti ndikuweruzeni ayi, pakuti ine ndanena kale kuti inu muli pamtima pathu, kufa nanu pamodzi, ndi kukhala ndi moyo pamodzi. 4Kulimbika mtima kwanga pa inu ndi kwakukulu, kudzitamandira kwanga ndi kwakukulu pofuna kukulemekezani; Ine ndadzala ndi chilimbikitso; ndapitilira kukondwa pansi pa m’sautso wathu. 5Pakutidi, pamene ife tinafika m’Makedoniya, thupi lathu silinapume konse, koma tinazunzika m’njira zonse; kunjaku zinthu zolimbana nazo, mkati mwathu kukhala ndi mantha. 6Koma Iye amene amalimbikitsa iwo amene ali odzichepetsa, [akhale] 2Mulungu, anatilimbikitsa ife pakubwera kwa Tito; 7ndipo osati kubwera kwake kokha, komanso kudzera mkulimbikitsidwa kumene Iye anakulimbikitsani nako; zokhudza ife monga mwa kukhumba kwanu, kulira kwanu, changu chanu pa ine; kotero kuti ine ndikakondwere koposa. 8Pakuti monga ndinalilira inu mu kalata muja, sindidandaula, ngakhale kuti ndinali wokhumudwa; pakuti ndiona kuti kalata ija, ngakhale kuti inali ya kanthawi kochepa, inakulizani. 9Tsopano ndikondwera, osati kuti mwamva chisoni kokha, koma kuti mwamva chisoni kufikira ku kulapa; pakuti inu mwamva chisoni cholinga kwa 3Mulungu, kuti musakhumudwitsidwe ndi ife. 10Pakuti chisoni cholinga kwa 4Mulungu chichita ku chipulumutso, osati chokhumudwitsa; koma chisoni cha dziko lapansi chichita imfa. 11Pakuti taonani, chinthu chomwechi, kumva chisoni kwanu kolinga kwa 5Mulungu, khama lalikulu bwanji linachitika mwa inu, koma [chimene]ichili chodzikonza [pa inu nokha], koma mkwiyo [wotani], koma mantha [otani], koma chikhumbokhumbo [chotani], koma kulimbika [kotani], koma kubwezera [kotani]: mu njira zonse mwaonetsa nokha kukhala angwiro m’menemo. 12chomwechonso, monga ndinalembera kwa inu, [sichinali] chifukwa cha iye amene anali wokhumudwayo, koma chifukwa cha kulimba mtima kwanu kumene kunaonekera pamaso pa 6Mulungu. 13Pachifukwa chimenechi ife talimbikitsidwa. Ndipo m’malo mwake tikondwera m’chilimbikitso chathu pa chifukwa cha chimwemwe cha Tito, chifukwa mzimu wake walimbikitsidwa ndi inu nonse. 14Chifukwa ngati ine ndinadzitamandira kwa iye kalikonse kokhudza inu, sindinachititsidwe manyazi; koma monga talankhula kwa inu zinthu zonse m’choonadi, chomwechonso kudzitamandira kwathu kwa Tito kwakhala choonadi; 15ndipo chikondi chake chichulukira kwa inu, pokumbukira kumvera kwa inu nonse, m’mene munamulandilira ndi mantha komanso nkuthunthumira. 167Ine ndikondwera kuti mu kalikonse ndakudalirani.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu