Mutu 5
1Koma pakuona khamulo, Iye anapita ku phiri, ndipo atakhala pansi, ophunzira ake anabwera kwa Iye; 2ndipo, pakutsegula pakamwa pake, Iye anawaphunzitsa iwo, nanena, 3Odala [ali] osauka mu mzimu, pakuti wao ndi ufumu wa kumwamba. 4Odala akubuma, pakuti iwo azatonthozedwa. 5Odala ali akufatsa, pakuti iwo adzalandira dziko lapansi. 6Odala iwo akumva njala ndi ludzu la chilungamo, pakuti iwo adzakhutitsidwa. 7Odala ali a chifundo, pakuti iwo adzapeza chifundo. 8Odala ali oyera mtima, pakuti iwo adzaona Mulungu1. 9Odala ali akuchita mtendere, pakuti iwo adzatchedwa ana a Mulungu2. 10Odala iwo akuzunzidwa chifukwa cha chilungamo, pakuti wao ndi ufumu wa kumwamba. 11Odala muli inu pamene adzanyadzitsa inu ndi kukuzunzani inu, nakunenerani zoipa zonse chifukwa cha Ine. 12Kondwerani ndi kusangalala, pakuti mphoto yanu ndi yaikulu kumwamba; pakuti iwo anazunza aneneri amene analipo inu musanabadwe.
13Inu ndinu mchere wa dziko lapansi; koma ngati mchere usukuluka, adzaukoleletsa ndi chiyani? Pamenepo usanduka wopanda ntchito koma kuti akautaye ndi kupondedwa ndi mapazi a anthu.
14Inu ndinu kuwala kwa dziko lapansi: mzinda womangidwa pamwamba pa phiri umene sungabisike. 15Kapenanso [anthu] samayatsa nyali ndi kuiyika kunsi kwa mbiya, koma amaiyika pa choikapo chake, ndipo imawalira iwo onse amene ali m’nyumbamo. 16Lolani nyali yanu iwalire anthu onse, kotero kuti akaone ntchito zanu za ngwiro, ndipo akalemekeze Atate wanu amene ali kumwamba.
17Musaganize kuti ndabwera Ine kudzapasula chilamulo kapena aneneri; Inetu sindinabwere kudzapasula, koma kudzakwaniritsa. 18Pakuti indetu ndinena kwa inu, Kufikira kumwamba ndi dziko lapansi zizapita, kalemba kakang’ono kamodzi kapena kansonga kake sikadzachoka mu chilamulo kufikira zonse zitakwaniritsidwa. 19Iye amene adzamasula limodzi la malamulo ang’onoang’ono awa, nadzawaphunzitsa anthu chomwecho, adzatchedwa wamng’ono mu ufumu wa kumwamba; komatu amene adzachita ndi kuwaphunzitsa [iwo], iye adzatchedwa wamkulu mu ufumu wa kumwamba. 20Pakuti ndinena ndi inu, kuti ngati kulungama kwanu sikuposa [kwa] alembi ndi Afarisi, simudzalowa konse mu ufumu wa kumwamba.
21Munamva inu kuti kunanenedwa kwa akalewo, Usaphe; koma iye wakupha ali woyenera chiweruzo. 22Koma Ine ndinena kwa inu, koma yense wakupsa mtima pang’ono ndi m’bale wake ali woyenera chiweruzo ; koma iye wakunena m’bale wake, wopanda pake, ali woyenera [kuitanidwa pamaso] pa sanihedrimu ; koma iye amene adzanena mzake kuti, Chitsiru, ali woyenera chilango cha gehena wa moto. 23Ngati mupereka mphatso yanu pa guwa, ndipo mwakumbukira kuti m’bale wanu ali nanu mangawa, 24Siyani pa guwa pomwepo mphatso yanuyo, ndipo yambani mwapita kukayanjanitsidwa ndi m’bale wanuyo, ndipo pamenepo perekani mphatso yanuyo. 25Fulumira kuyanjana ndi mzako wa mlandu, pamene uli naye panjira; kapena mzako wa mlandu angakupereke iwe kwa woweruza mlandu, ndi woweruzayo angakupereke iwe kwa msilikali, ndipo angakuponye iwe m’ndende. 26Indetu ndinena ndi iwe, sudzatulukamo m’menemo kufikira utalipira kakobiri komaliza.
27Munamva kunanenedwa, Musachite chigololo. 28Koma Ine ndinena kwa inu, iye wakuyang’ana mkazi mwa chilakolako ameneyo wachita kale chigololo ndi iye mu mtima mwake. 29Komatu ngati diso lako la manja likhala msampha kwa iwe, likolowole ndi kulichotsa kwa iwe: pakuti ndi kopindulitsa kwa iwe kuti chiwalo chimodzi chionongedwe, ndi kuti thupi lako lonse lisaponyedwe ku moto. 30Ndipo ngati dzanja lako lamanja likhala msampha kwa iwe, lidule ndi kulichotsa kwa iwe: pakuti ndi kopindulitsa kwa iwe kuti chiwalo chimodzi chionongeke, ndi kuti thupi lako lonse lisaponyedwe ku moto.
31Kunanenedwanso, amene adzachotsa mkazi wake, ampatse iye kalata wa chilekaniro. 32Komatu Ine ndinena kwa inu, kuti iye amene adzachotsa mkazi wake, osati chifukwa cha chigololo, ampangitsa iye kuchita chigololo, ndipo iye amene akwatira wotchotsedwayo wachita chigololo.
33Komanso, munamva kuti kunanenedwa kwa akalewo, usalumbire iwe wekha konama, koma udzipereka kwa Ambuye zolumbira zako. 34Komatu Ine ndinena kwa inu, musalumbire konse; kapena kutchula kumwamba, chifukwa ndiko kuli mpando wa chifumu wa Mulungu; 35kapena kutchula dziko lapansi, pakuti ndilo choponderapo mapazi ake; kapena kutchula Yerusalemu, chifukwa ndiwo mzinda wa mfumu yaikulukulu. 36Kapenanso usalumbire ku mutu wako, chifukwa sungapangitse tsitsi lako limodzi kuoneka loyera kapena lakuda. 37Komatu mau anu akhale, Inde, inde; Iyayi, iyayi; komatu chilichonse choonjezera pamenepa chichokera mu choipa.
38Munamva kuti kunanenedwa, Diso ku diso ndi Dzino ku dzino. 39Koma ndinena kwa inu musakanize choipa; koma iye amene adzamenya inu pa tsaya ladzanja lamanja, mpatseninso mbali inayo; 40ndipo kwa iye amene adzapita ku mlandu ndi iwe natenga malaya ako, msiyilenso chofunda chako. 41Ndipo amene adzakukakamiza iwe kumperekeza mtunda umodzi, mperekeze mitunda iwiri. 42Kwa iye amene akupempha iwe mpatse, ndipo kwa iye amene akhumba kubwereka kwa iwe usamkanize.
43Munamva kuti kunanenedwa, uzikonda mnansi wako ndi kumuda mdani wako. 44Koma ndinena kwa inu, kondani adani, [adalitseni iwo akutemberera inu,] achitireni zabwino iwo akudana ndi inu, ndipo apempherereni iwo [akunyoza inu ndi] kuzunza inu, 45kuti mukakhale ana a Atate wanu amene ali kumwamba; pakuti Iye amawalitsa dzuwa pa oipa ndi abwino, ndi kugwetsa mvula pa olungama ndi osalungama omwe. 46Pakuti ngati mukonda iwo akukonda inu, kodi mphoto yanu ndi chiyani? Kodi ngakhale okhometsa msonkho samachita chimodzimodzi? 47Kodi ngati mulonjerana ndi abale anu okha, ndi chiyani mukuchita chapadera choposa ena? Kodi Amitundu samachitanso chimodzimodzi? 485Chomwecho inu khalani angwiro monga Atate wanu wakumwamba ali wangwiro.
1Elohimu 2Elohimu