Mutu 3
1Ndipo Iye analowanso m’sunagoge; ndipo pamenepo panali munthu amene anali wopuwala dzanja. 2Ndipo iwo anamuyang’anira Iye ngati adzamuchiritsa pa sabata, kuti akamupezere mlandu. 3Ndipo Iye anati kwa munthu amene anali wopuwala dzanja, Tadzuka [ndipo ubwere] pakatipa. 4Ndipo Iye anati kwa iwo, Kodi ndi kololedwa tsiku la sabata kuchita zabwino kapena zoipa, kupulumutsa moyo kapena kupha? Komatu iwo anakhala chete. 5Ndipo pamene anawaunguza iwo ndi mkwiyo, ndi kukhudzika chifukwa cha kuuma kwa mitima yawo, Iye anati kwa munthuyo, Tambasula dzanja lako. Ndipo iye analitambasula [ilo], ndipo dzanja lake linabwenzeretsedwa. 6Ndipo Afarisi potuluka panja nthawi yomweyo ndi Aherode anakhala upo wakutsutsana naye, m’mene iwo angamuonongere Iye.
7Ndipo Yesu anachokapo pamodzi ndi ophunzira ake napita kunyanja; ndipo khamu lalikulu lochokera ku Galileya linamlondola Iye, ndi laku Yudeya, 8ndi laku Yerusalemu, ndi laku Idumeya ndi kupyola ku Yordano; ndiponso iwo ochokera ku Turo ndi Sidoni, khamu lalikulu, pakumva zinthu zazikulu zimene Iye anazichita, anabwera kwa Iye. 9Ndipo Iye analankhula kwa ophunzira ake, cholinga kuti kangalawa kamdikire Iye chifukwa cha khamulo, kuti iwo asamukanikize Iye. 10Pakuti Iye anachiritsa ambiri, kotero kuti iwo anamukanikiza kuti amukhudze, onse amene anali ndi zowawa. 11Ndipo mizimu yoipa, m’mene inamuona Iye, inamgwadira, nifuula kuti, Ndinu Mwana wa Mulungu1. 12Ndipo Iye anaidzudzula iyo kwambiri, kuti isamuulule.
13Ndipo Iye anakwera kupita ku phiri, ndipo anaitana iwo amene anawafuna, ndipo iwo anapita kwa Iye. 14Ndipo Iye anasankha anthu khumi ndi awiri kuti akhale naye, ndipo kuti akawatume iwo kukalalikira, 15ndi kukhala ndi mphamvu [ya kuchiritsa matenda, komanso] kutulutsa ziwanda. 16Ndipo Iye anamupatsa Simoni dzina lina lakuti Petro; 17ndi Yakobo [mwana] wa Zebedayo, ndi Yohane m’bale wake wa Yakobo, ndipo Iye anawapatsa iwo dzina lakuti Boanerge, ndiko kutanthauza, Ana a bingu; 18ndi Andreya, ndi Filipo, ndi Bartolomeyo, ndi Mateyu, ndi Tomasi, ndi Yakobo [mwana] wa Alifeyo, ndi Tadeyo, ndi Simoni m’Kanani, 19ndi Yudase Isikariote, amenenso anampereka Iye. Ndipo iwo analowa m’nyumba.
20Ndipo anthu ambiri anasonkhananso, kotero kuti iwo sanathe kudya ndi mkate womwe. 21Ndipo abale ake atamva [za ichi] anatuluka kuti akamugwire Iye, pakuti iwo anati, wazungulira mutu, 22Ndipo alembi amene anabwera kuchokera ku Yerusalemu anati, Ali ndi Beelzibule, ndipo ndi mkulu wa ziwanda Iyeyu amatulutsa ziwandazo. 23Ndipo atawaitana iwo kwa [Iye], ananena nawo m’mafanizo, Kodi Satana akhoza kutulutsa Satana? 24Ndipo ngati ufumu ugawanika paokha, ufumu umenewo sungakhazikike. 25Ndipo ngati nyumba igawanika pa iyo yokha, nyumba imeneyo singakhazikike. 26Ndipo ngati Satana aziukira iye mwini, ndipo wagawanika, iye sangakhazikike, ndipo atsirizika. 27Komatu palibe amene, angalowe m’nyumba yake, kusakaza katundu wa [munthu] wa mphamvu pokhapokha ngati ayamba kumanga [munthu] wa mphamvuyo, pamenepo azasakaza katundu wake. 28Indetu ndinena kwa inu, kuti machimo onse adzakhululukidwa kwa ana a anthu, ndiponso mau onse achipongwe [amene] adzawalankhula mwachipongwe; 29koma aliyense wakulankhula mwachipongwe Mzimu Woyera, kwamuyaya sadzakhululukidwa; komatu adzakhala pansi pa kutsutsika kwa tchimo lamuyaya; 30chifukwa iwo anati, Iye ali ndi mzimu woipa.
31Ndipo abale ake ndi mayi wake anafika, atayima panja natuma uthenga wa kumuitana Iye. 32Ndipo khamu linakhala pomzungulira Iye. Ndipo anati kwa Iye, Taonani, mayi wanu ndi abale anu akukufunani panja. 33Ndipo Iye anawayankha iwo, nanena, Mayi wanga ndi ndani kapena abale anga ndi ndani? 34Ndipo pakuwunguza iwo amene anakhala pomzungulira Iye, anati, Taonani mayi wanga ndi abale anga: 35pakuti aliyense wakuchita chifuniro cha Mulungu2, ameneyo ndiye m’bale wanga, ndi mlongo wanga, ndi mayi wanga.
1Elohimu2Elohimu