Mutu 25

1Pamenepo Festo, analowa m’dziko lake, pakutha pa masiku atatu anakwera ku Yerusalemu kuchokera ku Kaisareya. 2Ndipo akulu ansembe ndi mkulu wa Ayuda anam’neneza Paulo kwa iye, ndipo anamdandaulira iye, 3napempha monga chisomo kutsutsana naye kuti amtumize ku Yerusalemu, nayika anthu panjira kuti amuphe. 4Pamenepo Festo anayankha kuti Paulo asungidwe ku Kaisareya, ndi kuti iye mwini adzanyamuka posachedwa. 5Pamenepo lolani anthu a ulamuliro pakati panu, atero iye, atsikirenso nawo, ngati pali kanthu mwa munthu uyu, mnenezeni iye. 6Ndipo atatsalira nawo podutsa masiku asanu ndi atatu kapena khumi, anatsikira iye ku Kaisareya; ndipo tsiku lotsatiralo, anakhala pa mpando woweruza, nalamulira kuti abwere naye Paulo. 7Ndipo pamene anabwera, Ayuda amene anatsika kuchokera ku Yerusalemu anayima mozungulira, ndipo anabweretsa milandu ikuluikulu imene analibe nayo umboni: 8Paulo anadziyankhira yekha, Sindinachimwire lamulo kapena Ayuda, kapena kachisi, kapena Kaisara, sindinalakwe mwa mtundu wina ulionse. 9Koma Festo, pofuna kusangalatsa Ayuda, kupeza kukonderedwa mwa iwo, anamuyankha Paulo nati, Kodi uli wokonzeka kukwera kupita ku Yerusalemu, kuti kumeneko ukaweruzidwe pamaso panga zokhudza zinthu izi? 10Koma Paulo anati, Ine ndayimilira pamaso pa mpando wa chiweruzo wa Kaisara, pamenepo ndikuyenera kuweruzidwa. Kwa Ayuda palibe cholakwa ndachita, monga inunso mukudziwa bwino. 11Pamenepo ngati ndachita kalikonse kolakwa ndipo ndachita kanthu koyenera kuphedwa nako, sindikukana kuphedwa; koma ngati palibe ndachita koipa pa zinthu izi akundineneza, palibe munthu adzandipereka kwa iwowa. Ndidandaulira kwa Kaisara. 12Pamenepo Festo, atakambitsana ndi akulu abwalo, anayankha, Wadandaulira kwa Kaisara. Kwa Kaisara udzapita. 13Ndipo pamene anadutsa masiku angapo, Agripa mfumuyo ndi Bernike anafika ku Kaisareya kudzamlonjera Fetso. 14Ndipo pamene iwo anakhala masiku ambiri kumeneko, Festo anatula m’manja mwa mfumuyo nkhani yokhudza Paulo, nanena, Pali munthu wina wandende amene anasiyidwa m’ndende ndi Felike, 15amene ine pamene ndinali ku Yerusalemu, akulu ansembe ndi akulu a Ayuda anam’neneza mlandu, wofunika kuti aweruzidwe iye: 16kwa iwo ndinawayankha, Sichikhalidwe cha Chiroma kupereka munthu asanakumane ndi iwo amene akumtsutsa maso ndi maso, ndi kukhala ndi mwayi wodziteteza pokhudza mlanduwo. 17Pamenepo iwo atakumana pamodzi, posafuna kuchotsa mlanduwo, ndinakhala pa mpando woweruza ndi kulamulira munthuyu kuti abweretsedwe: 18zokhudza iwo omnenezawo, poyimilira, sanabweretse chom’tsutsa monga mwa chiyembekezo changa; 19koma anamfunsa iye mafunso okhudza kayendetsedwe ka chipembedzo, komanso zokhudza Yesu wina amene anafa, amene Paulo akutsimikizira kuti ali moyo. 20Ndipo monga mwa ine mwini ndinasowa kafukufuku wa zinthu izi, ndinati, Anali wokonzeka kupita ku Yerusalemu kukaweruzidwa zokhudza zinthu izi? 21Koma Paulo anapempha kuti asungidwe kuonekera pamaso pa Augusto, ine ndinalamulira iye kuti asungidwe kufikira ndidzamtumiza kwa Kaisara. 22Ndipo Agripa [anati] kwa Festo, Inenso ndikufuna nditamumva munthu ameneyu. Mawa mudzamumva munthu ameneyu, anatero iye.

23Pamenepo iye m’mawa mwake, atafika Agripa, ndi Bernike, ndi ulemelero waukulu, ndipo atalowa momvera milandu, pamodzi ndi akapitawo akulu ndi anthu otchuka a mumzindamo, ndipo Festo anapereka ulamuliro, Paulo anabweretsedwa. 24Ndipo Festo anati, Mfumu Agripa, ndi anthu onse amene muli pano, mukumuona munthu uyu, amene khamu lonse la Ayuda anapempha kwa ine ku Yerusalemu ndi kuno komwe, nafuula motsutsana [naye] kuti sakuyenera kukhala ndi moyo. 25Koma ine, poona kuti iye sanachite kolakwa koyenera kufa, ndipo munthu uyu podandaulira kwa Augusto, ndaganiza kuti ndimtumize iye; 26ameneyu ine ndilibe kanthu koyenera kulembera mbuye wanga. Pamenepo ine ndam’bweretsa kwa inu, ndipo makamaka pamaso panu, mfumu Agripa, kuti mwina pamene wafunsidwa ndidzakhala nako kolemba: 27pakuti zikuoneka zopanda pake kwa ine, kumtumiza ku ndende, osaonetsera mlandu wotsutsana naye.