Mutu 4
1Koma Yesu, wodzala ndi Mzimu Woyera, anabwera kuchokera ku Yordano, ndipo anatsogozedwa ndi Mzimu m’chipululu 2masiku makumi anayi, nayesedwa ndi mdierekezi; ndipo masiku amenewo sanadye kanthu, ndipo pamene anamaliza kusala kudya Iye anamva njala. 3Ndipo mdierekezi anati kwa Iye, ngati ndiwe Mwana wa Mulungu1, lankhula kwa mwala uwu, kuti usanduke mkate. 4Ndipo Yesu poyankha anati kwa iye, Kwalembedwa, munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, komatu ndi mau a Mulungu2.
5Ndipo [mdierekezi], anamtsogolera Iye pamwamba pa phiri lalitali, namuonetsa maufumu onse okhalapo padziko lapansi, mu kanthawi kochepa. 6Ndipo mdierekezi anati kwa Iye, Ine ndidzakupatsa mphamvu zonse izi, ndi ulemelero wake; pakuti zinapatsidwa kwa ine, komanso kwa aliyense amene ine ndifuna ndidzampatsa. 7Ngati Iwe udzandiIambira pamaso panga, [onsewu] udzakhala wako. 8Ndipo Yesu pomuyankha iye anati, Kwalembedwa, udzimlambira Ambuye Mulungu3 wako, ndipo Iye yekha udzimtumikira.
9Ndipo anamtsogolera Iye ku Yerusalemu, namuika Iye pamwamba pa kachisi, nati kwa Iye, Ngati ndiwe Mwana wa Mulungu4, ziponye wekha pansi; 10pakuti kwalembedwa, Iye adzalamulira angelo ake zokhudza iwe kukuteteza; 11ndipo m’manja [mwao] adzakunyamula, kuti phazi lako lisaponde mwala. 12Ndipo Yesu pomuyankha anati kwa iye, Kunanenedwa, Usamuyese Ambuye Mulungu5 wako.
13Ndipo mdierekezi, atamaliza yesero lililonse, anachoka kwa Iye mwa kanthawi.
14Ndipo Yesu anabwerera mu mphamvu ya Mzimu ku Galileya; ndipo mphekesera yokhudza Iye inapita kumaiko onse ozungulira; 15ndipo Iye anaphunzitsa m’masunagoge awo, nalemekezedwa ndi onse.
16Ndipo Iye anabwera ku Nazareti, kumene analeredwa; ndipo Iye analowa, monga mwa chizolowezi, m’kachisi patsiku la sabata, ndipo anaimirira kuwerenga. 17Ndipo buku la mneneri Yesaya linapatsidwa kwa Iye; ndipo atafunyulula bukulo anapeza malo amene panalembedwa, 18Mzimu wa Mulungu uli pa ine, chifukwa wandidzodza ine kulalikira uthenga wabwino kwa osauka; wandituma ine kukalalikira mamasulidwe kwa amsinga, ndi kwa akhungu kupenyaso, kutulutsa ndi ufulu ophwanyika, 19kulalikira chaka chovomerezeka cha Ambuye. 20Ndipo pamene analipinda bukulo, analipereka kwa mnyamata, nakhala pansi; ndipo maso a anthu onse mkachisimo anali pa Iye. 21Ndipo Iye anayamba kulankhula nawo, Lero lemba ili lakwaniritsidwa m’makutu mwanu. 22Ndipo anthu onse anamchitira umboni Iye, ndipo anali odabwa ndi mau a chisomo amene amatuluka mkamwa mwake. Ndipo iwo anati, Kodi uyu simwana wa Yosefe? 23Ndipo Iye anati iwo, Inutu mudzanena kwa Ine fanizo ili, Sing’anga, udzichiritse wekha; zilizonse zimene tinazimva kuti zinachitika ku Kapernao, upangenso zimenezo m’dziko lako lino. 24Ndipo Iye anati, Ndithudi ndinena kwa inu, kuti palibe mneneri amene amalandiridwa m’dziko lake [lomwe]. 25Komatu mwa choonadi Ine ndinena kwa inu, Analiko akazi amasiye ambiri m’masiku a Eliya, pamene kumwamba kunatsekeka kwa zaka zitatu ndi miyezi isanu ndi umodzi, kotero kuti njala yaikulu inabwera padziko lonse, 26ndipo Eliya sanatumidwe kwa aliyense wa iwo komatu anatumidwa kwa Sarepta wa ku Sidoniya, kwa mkazi [amene anali] wa masiye. 27Ndipo analiko akhate mu Israyeli m’masiku a Elisa mneneri, ndipo palibe wa iwo amene anachiritsidwa koma Namani wa ku Suriya. 28Ndipo iwo onse anadzadzidwa ndi mkwiyo m’sunagogemo, pakumva zinthu zimenezi; 29ndipo ponyamuka iwo anamtulutsa Iye kunja kwa mzinda, napita naye pamwamba pa phiri pamene mzinda wawo unamangidwa, cholinga kuti akamuponye Iye pansi kuphompho; 30koma Iye, podutsa pakati pawo, anawachokera.
31Ndipo anatsikira ku Karpenao, mzinda wa Galileya, ndipo anawaphunzitsa pa sabata. 32Ndipo iwo anali ozizwa ndi chiphunzitso chake, pakuti mau ake anali ndi ulamuliro. 33Ndipo analiko munthu wina m’sunagoge amene anali ndi mzimu wa chiwanda choipa, ndipo iye anafuula ndi mau okweza, 34nanena, Ha! Kodi tidzachita chiyani ndi Inu, Yesu, m’Nazarayo? Kodi mwabwera kudzationonga ife? Inetu ndikudziwani Inu, Woyerayo wa Mulungu1. 35Ndipo Yesu anamdzudzula iye, nanena, Ukhale chete, ndipo tuluka mwa iye. Ndipo chiwandacho, pomugwetsa iye pansi pakati pawo, chinatuluka mwa iye popanda kumuvulaza. 36Ndipo kudabwa kunawafikira onse. Ndipo analankhula kwa wina ndi mzake, nanena, Mau awa ndi otani? Pakuti ndi ulamuliro komanso mphamvu Iye akungolamula mizimu yoipa, ndipo ikungotuluka. 37Ndipo mphekesera yokhudza Iye inazungulira malo onse a mdzikomo.
38Ndipo potuluka m’sunagoge, Iye analowa m’nyumba ya Simoni. Komatu mpongozi wake wa Simoni amadwala malungo akulu; ndipo anampempha Yesu za iye. 39Ndipo Yesu poyimilira pafupi ndi iye, anadzudzula malungowo, ndipo anamuleka iye; ndipo pomwepo anayimilira nawatumikira iwo.
40Ndipo pamene dzuwa linali kulowa, onse, amene anali ndi anthu odwala nthenda zosiyanasiyana, anawabweretsa kwa Iye, ndipo posanjika manja ake pa aliyense wa iwowa, anawachiritsa iwo; 41ndipo ziwanda zinatuluka mwa anthu ambiri, akulira nanena, Ndinu mwana wa Mulungu2. Ndipo pozidzudzula izo, Iye anazikaniza kuti zisalankhule, pakuti zinamudziwa Iye kuti ndi Khristu.
42Ndipo pamene kunacha Iye anatuluka, napita kumalo a chipululu, ndipo khamulo linamsakasaka Iye, ndipo anampeza, ndipo iwo anayesa kumletsa Iye kuti asawachokere. 43Koma Iye anati kwa iwo, Inetu ndikuyenera kukalika uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu3 ku mizindanso ina, pakuti chimenechi ndi chomwe ndinatumidwa. 44Ndipo Iye anali kulalikira m’sunagoge ya ku Galileya.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu