Mutu 16
1Tsopano zokhudza chopereka cha oyera mtima, monga ndinalangizira mipingo yaku Galatiya, chomwecho muchitenso inu. 2Patsiku loyamba la sabata aliyense wa inu azipatula kunyumba kwake, kalikonse molingana ndi mlingo wa kupeza kwake, kuti pasachitike chopereka ine ndikabwera. 3Ndipo pamene ine ndifika, aliyense amene mwamuyenereza, zimenezi ndidzatumiza pamodzi ndi kalata atenge mphatso yanu kupita nayo ku Yerusalemu: 4ndipo ngati nkoyenera kuti ndipite, adzapita pamodzi ndi ine. 5Koma ine ndidzabwera kwa inu pamene ndidzadutsira ku Makedoniya. 6Koma mwina ndidzakhala ndi inu, mwinanso nyengo yozizira, kuti muwakonzekeretse iwo amene ndidzapita nawo. 7Pakuti sindidzakuonaninso mwa kanthawi, pakuti ndikuyembekezera kukhala nanu kwa nthawi, ngati Ambuye alola. 8Koma ndikhalabe mu Efeso kufikira Pentekoste. 9Pakuti khomo lalikulu latsegukira ine ndiyo ntchito ya phindu, ndipo otsutsana nane alipo ochuluka.
10Tsopano ngati Timoteo afika, onetsetsani kuti akhale nanu popanda mantha; pakuti iye akugwira ntchito ya Ambuye, monga inenso. 11Pasapezeke munthu womuchepetsa iye; koma mtumizeni mu mtendere, kuti abwere kwa ine; pakuti ndikumuyembekezera iye ndi abale ena. 12Tsopano zokhudza m’bale Apolo, ndinam’dandaulira kwambiri kuti abwere kwa inu ndi abale ena; koma sichinali chifuniro chake kupita tsopano; koma adzabwera akapeza mpata wabwino. 13Limbani mtima; chilimikani m’chikhulupiliro; zikhazikeni ngati amuna; khalani a mphamvu. 14Zinthu zonse zimene muchita chitani m’chikondi.
15Koma ndikupemphani, abale, (inu mudziwa nyumba ya Stefano, kuti ndi chipatso choyamba cha Akaya, ndipo iwo anadzipereka okha kwa oyera mtima mkutumikira,) 16kuti inunso mudziwamvera anthu oterewa, ndi onse amene analowa mu ntchitoyi ndi kudzipereka. 17Koma ndisangalala ndi kubwera kwa Stefano ndi Fortunato ndi Akaya; chifukwa iwowa anapereka zimene zimasowekera kumbali yanu. 18Pakuti iwo atsitsimutsa mzimu wanga ndi mzimu wanu: alemekezeni oterewa. 19Mipingo yaku Asiya ikukulonjerani. Akwila ndi Priska, ndi mpingo wosonkhana m’nyumba zawo, akukulonjerani zedi mwa Ambuye. 20Abale onse akukulonjerani. Lonjeranani wina ndi mzake ndi chipsopsono choyera.
21Malonje a ineyo Paulo ndi manja anga omwe. 22Ngati wina sakonda Ambuye [Yesu Khritu] akhale wotembereredwa akudza Ambuye. 23Chisomo cha Ambuye Yesu chikhale ndi inu. 24Chikondi changa chikhale ndi inu nonse mwa Yesu Khristu. Amen.